Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 27, 2020
UNITED STATES

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2020—ku United States

Nkhani ya Chikumbutso Inaulutsidwa M’ndende Ziwiri ku Florida

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2020—ku United States

Madzulo a pa 7 April, nkhani ya Chikumbutso yojambulidwa kale inaulutsidwa m’ndende ziwiri ku Palm Beach County, Florida. Akaidi oposa 1,100 anamvetsera nkhaniyi ngakhale kuti kundendezi kunalibe wa Mboni aliyense woti akachititse mwambowu.

Mmodzi wa abale 12 amene amapita kundendezi kukalalikira mlungu uliwonse ananena kuti: “Zinatidabwitsa kwambiri kuona mmene zinthu zinayendera bwino. N’zosachita kufunsa kuti Yehova ndi amene anachititsa kuti anthuwa amvetsere nawo nkhani ya Chikumbutso.”

Abalewo anali atapempha wansembe wa kundendeko ngati angawapatse chilolezo choti adzachite mwambo wa Chikumbutso m’ndende ziwirizi. Koma boma litaika lamulo loletsa kuyenda chifukwa cha mliri wa COVID-19, abalewo analephera kupitako. Abalewo ali mkati moganizira njira ina, anadabwa wansembeyo akuwapempha kuti amupatse nkhani yojambulidwa kale ya Chikumbutso. Wansembeyo anali atakonzeka kale kuulutsa nkhaniyo m’ndende ziwiri zonsezo.

Kuwonjezera pa vidiyoyo, abalewo anakonza zoti atumizirenso wansembeyo timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso, kuti akagawire akaidi kapena akamate m’ndendezo m’malo oti anthu atha kuwerenga. Apanso abalewo anadabwa kwambiri kumva kuti wansembeyo anali atamata kale m’makoma a ndendezo chidziwitso choitanira anthu ku nkhani ya Chikumbutso. Madzulo a tsiku la Chikumbutso, mkaidi aliyense anali ndi mwayi woti atha kuonera nkhani yochokera m’Baibuloyi.

Pambuyo pa tsiku limeneli, wansembeyo anapempha abalewo kuti abweretse Mabaibulo enanso oti adzapatse akaidiwo chifukwa Mabaibulo onse omwe anali kundendezi anali atagawidwa kale. Ndipotu chiwerengero cha Mabaibulo omwe anapemphedwawo chinali chachikulu kwambiri.

Tikusangalala kudziwa kuti palibe ndende imene ingalepheretse kuti Mawu a Mulungu afikire anthu.—Mateyu 24:14.