Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 19, 2019
UNITED STATES

Mwana Wasukulu Waombera Anzake ku California M’dziko la United States

Mwana Wasukulu Waombera Anzake ku California M’dziko la United States

Pa 14 November, 2019, mwana wasukulu wina anaombera anzake a m’kalasi pasukulu ina mumzinda wa Santa Clarita ku California. Mnyamatayu anapha ana asukulu awiri ndipo atatu anavulala kenako anadziombera.

N’zomvetsa chisoni kuti mwana wamwamuna wa mlongo wathu wina dzina lake Dominic Blackwell, ndi mmodzi mwa ana asukulu omwe anaphedwa. Dominic anali ndi zaka 14 ndipo ankasonkhana mokhazikika ndi mayi ake, Mlongo Nancy Blackwell. Iye wasiya makolo ndi azibale ake atatu. Akulu akugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo potonthoza komanso kuthandiza banjali ndi mpingo.

Tili ndi chisoni chachikulu chifukwa cha imfayi. Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene Mulungu “adzapukuta misozi yonse . . . , ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:4.