Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Alendo akuona malo osungirako zinthu zakale ku Warwick pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono zomwe zimaonetsa mavidiyo a m’Chinenero Chamanja cha ku America.

FEBRUARY 11, 2019
UNITED STATES

Nkhani Zofotokozera Zinthu Zakale ku Likulu Lathu Lapadziko Lonse Tsopano Zilinso M’chinenero Chamanja cha ku America

Nkhani Zofotokozera Zinthu Zakale ku Likulu Lathu Lapadziko Lonse Tsopano Zilinso M’chinenero Chamanja cha ku America

Kuyambira mu January 2019, nkhani zofotokozera zinthu zakale zomwe zili ku likulu lathu lapadziko lonse zinayamba kupezekanso m’Chinenero Chamanja cha ku America. A Enrique Ford omwe amayang’anira Dipatimenti Yosunga Zinthu Zakale anati: “Ntchito yomasulira komanso yopanga mapulogalamu a pa kompyuta yomwe inathandiza kuti nkhani zofotokozera zinthu zakale zikhale m’Chinenero Chamanja cha ku America, inali yochititsa chidwi kwambiri. Panopa abale ndi alongo omwe ali ndi vuto losamva akabwera kudzaona zinthu zakalezi, azisangalala komanso kupindula kwambiri.”

Ana Barrios, yemwe ali ndi vuto losamva ndipo amatumikira monga mpainiya wokhazikika ku New York, anali m’gulu la anthu oyamba kukaona zinthu zakale zofotokozedwa m’Chinenero Chamanja cha ku America. Iye anati: “Ndinasangalala kwambiri atandipatsa chipangizo chokhala ndi mavidiyo a m’Chinenero Chamanja cha ku America. Ngakhale kuti m’mbuyomu ndinapitanso kumalo osungira zinthu zakalewa ndipo ndinkadziwa zinthu zomwe ziliko, mfundo zokhudza zinthuzo zinali zisanandifikebe pamtima chifukwa kungowerenga mawu m’Chingelezi ofotokozera zinthuzo sikunandithandize kumvetsa bwinobwino. Nditaonera mavidiyo angapo a m’Chinenero Chamanja cha ku America, ndinayamba kumvetsa bwino dzina la Yehova kuposa m’mbuyo monsemu. Zomwe ndinaonazo zinafotokoza kwambiri zinthu zosiyanasiyana zokhudza makhalidwe a Yehova ndipo zimenezi zinandikhudza kwambiri mpaka ndinalira.”

Ntchito yoti pakhale mavidiyo ofotokozera zinthu zakale m’Chinenero Chamanja cha ku America inayamba mu June 2017. Abale ndi alongo okwana 23 kuphatikizapo ofalitsa 6 omwe ali ndi vuto losamva ndi enanso 6 omwe alibe vutoli koma anakula ndi makolo a vuto losamva, anathandiza nawo pa ntchito yomasulira komanso yokonza mavidiyo m’Chinenero Chamanja cha ku America. Gulu la omasulirawa linajambula mavidiyo oposa 900 omwe kuwaphatikiza ndi a maola pafupifupi 9, kuti agwirizane ndi mawu ojambulidwa ofotokozera zinthu zomwe zili m’malo osungira zinthu zakalewa. Ntchito yojambula mavidiyo ofotokozera zinthu zakale m’Chinenero Chamanja cha ku America inachitikira m’masitudiyo omwe ali m’malo atatu awa: Ofesi ya omasulira zinthu za m’Chinenero Chamanja cha ku America ya mumzinda wa Fort Lauderdale ku Florida, maofesi a Mboni za Yehova a ku United States omwe ali m’tawuni ya Wallkill ku New York, ndiponso maofesi a kulikulu lapadziko lonse m’tawuni ya Warwick ku New York. Asanatulutse mavidiyowa, abale ndi alongo a vuto losamva azaka zosiyanasiyana komanso ochokera m’madera osiyanasiyana, anawaonera kaye komanso anathandiza nawo pa ntchito yoonetsetsa kuti awamasulira m’njira yoti anthu oyankhula Chinenero Chamanja cha ku America azisangalala akapita kukaona malowa.

Ena mwa abale ndi alongo amene anathandiza nawo popanga mavidiyo a m’Chinenero Chamanja cha ku America ofotokozera zomwe zili kumalo osungirako zinthu zakale.

Dipatimenti Yosunga Zinthu Zakale inagula zipangizo zamakono zomwe zimaonetsa mavidiyo a m’Chinenero Chamanja cha ku America ofotokozera zomwe zili kumalo osungirako zinthu zakalewa. Zipangizozi zimagwira ntchito mofanana ndi mmene zipangizo zomwe zili ndi mawu ojambulidwa ofotokozera zinthuzi zimachitira. Dipatimentiyi inapanganso zoti masikirini 14 omwe anali kale m’malo osungira zinthu zakalewa azitha kuonetsa mavidiyo a m’Chinenero Chamanja cha ku America.

A Mark Sanderson a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anati: “Cholinga cha malo osungira zinthu zakale a ku Warwick ndi kulimbikitsa komanso kulimbitsa chikhulupiriro cha anthu onse omwe amabwera kudzaona likulu la padziko lonse. Ndife osangalala kuti nkhani zofotokozera zinthu zakale zayamba kupezeka m’zinenero 14, kuphatikizapo m’Chinenero Chamanja cha ku America. Zimenezi zithandiza abale ndi alongo ngakhalenso anthu omwe si Mboni amene ali ndi vuto losamva.”

Pofika pano, alendo oposa 500,000 anakaona likulu lathu ku Warwick. Tikulimbikitsa abale ndi alongo padziko lonse lapansi kuti abwere ndi kudzadzionera okha malo osungirako zinthu zakalewa ndipo adzadziwa zambiri zokhudza mbiri ya Mboni za Yehova. Onse amene adzabwere adzalimbikitsidwa kuti apitirize ‘kudalira Mulungu.’—Salimo 78:7.

Pokonzekera tsiku lodzayamba kugwiritsa ntchito nkhani zofotokozera zinthu zakale m’Chinenero Chamanja cha ku America, m’bale akuonera vidiyo ku likulu lathu lapadziko lonse ku Warwick, New York, pofuna kutsimikizira kuti ili bwino.

Ana atatu omwe makolo awo ali ndi vuto losamva akuonera sewero la nkhani ya m’Baibulo m’Chinenero Chamanja cha ku America ya m’chaka cha 1977, yomwe inali ndi mutu wakuti “Dzina la Yehova Liyenera Kulengezedwa pa Dziko Lonse Lapansi.”

Gulu la abale ndi alongo akuona zinthu zakale pambali yakuti “Dzina la Mulungu M’Baibulo” pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono.

Alendo akuonera vidiyo ya m’Chinenero Chamanja cha ku America pa sikirini kumalo osungirako zinthu zakale pambali yakuti “Anthu Odziwika ndi Dzina la Yehova.”

Gulu la anthu oona malo akuonera vidiyo ya m’Chinenero Chamanja cha ku America yofotokozera zithunzi 500 za “Sewero la Pakanema la Chilengedwe.”