APRIL 22, 2020
UNITED STATES
“Nyumba ya Ufumu” Yoyambirira Yaperekedwanso kwa Yehova Patatha Zaka 85
M’bale Joseph F. Rutherford, yemwe pa nthawiyo anali pulezidenti wa Watch Tower Society, analipo pamene ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu yoyambirirayi inkayamba mu 1935. Nyumbayi ili ku 1228 Pensacola Street, mumzinda wa Honolulu ku Hawaii. Nyumbayi ndi yapadera chifukwa choti inali yoyamba padziko lonse kudziwika ndi dzina lakuti “Nyumba ya Ufumu.” Kwa zaka zoposa 80 tsopano, anthu ambimbiri akhala akulambira Yehova m’Nyumba ya Ufumu imeneyi. Panopa padutsa zaka 85 kuchokera pamene inamangidwa ndipo mumasonkhana mipingo 4. Misonkhano imachitika m’zinenero 5 kuphatikizapo m’Chihawaii Pidgin. a
Mliri wa COVID-19 usanabuke, abale anaitanira akuluakulu a boma, aphunzitsi ndi mapulofesa ku chionetsero cha Nyumba ya Ufumuyi yomwe inali atangoimaliza kuikonzanso. Chionetserochi chinachitika kuyambira pa 11 mpaka pa 15 February, 2020. Alendowa anaonetsedwa nyumbayi, anaona zinthu zosonyeza mbiri yokhudza nyumbayi komanso anamvetsera pamene abale ankafotokoza ntchito zomwe a Mboni za Yehova amagwira. Pa 16 February, M’bale David H. Splane, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anakamba nkhani yotseguliranso nyumbayi.
Mlongo wina yemwe anathandiza nawo pa ntchito yokonzekera chionetserochi, anati: “Ngakhale kuti sitinaitane anthuwa kuti tidzawalalikire, tikuona kuti ambiri adziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova ndipo mwina akanapanda kufika, sakanatha kupeza mwayi umenewu.”
Chionetserochi chinathandizanso abale ndi alongo athu kumvetsa bwino mbiri yochititsa chidwi yokhudza Mboni za Yehova m’zilumba za ku Hawaii ndipo anaona okha kukwaniritsidwa kwa mawu akuti, “M’zilumba zakunyanja adzalemekeza dzina la Yehova, Mulungu wa Isiraeli.”—Yesaya 24:15.
a Pamene kuli mliri wa COVID-19, mipingo yonse ku United States ikumasonkhana kudzera pa vidiyokomfelensi m’malo mosonkhana m’Nyumba za Ufumu.