Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

11 MARCH, 2021
UNITED STATES

Ulaliki Wamakalata Ukupitirizabe Kuthandiza Anthu

Ulaliki Wamakalata Ukupitirizabe Kuthandiza Anthu

A Mboni za Yehova ambiri akusangalala kugwira ntchito yolalikira polemba makalata. Nkhani zotsatirazi zochokera ku United States, zikusonyeza momwe njira imeneyi ikuthandizira kwambiri kufalitsa uthenga wolimbikitsa wochokera m’Baibulo.

Mlongo Carlee Ruggles limodzi ndi mayi ake akufufuza malemba oti aike mu makalata omwe akulemba

Mlongo Carlee Ruggles ali ndi zaka 13 ndipo amakhala mumzinda wa Blue Ash, ku Ohio. Iye anazindikira kuti ulaliki wamakalata ndi wothandiza kwambiri chifukwa cha zimene zinachitika ndi imodzi mwa makalata amene analemba.

Madzulo a tsiku lina Carlee ali panja pa nyumba yawo, anangoona munthu wina wa njinga ya moto akulowa mumsewu wobwera kunyumba yawo. Munthuyo anatsika panjingapo n’kufunsa kuti, “Wanditumizira kalata iyi ndani?” Carlee anazindikira kuti kalatayo inali ndi imodzi mwa makalata amene analemba pomwe ankagwira ntchito yolalikira.

Choncho, Carlee anayankha molimba mtima kuti, “Ndine amene ndinalemba.” Panthawiyi n’kuti makolo ake akufika pomwe iye anali.

Carlee komanso makolo akewo anadabwa pomwe munthuyo ananena kuti, “Chinthu chimene ndimafunikira kwambiri ndi kalata yakoyi.” Kenako munthuyo anafotokoza mmene kalatayo inamulimbikitsira pamene anali ndi nkhawa pomwe anakaona kuti ali yekhayekha chifukwa cha mliriwu. Anafotokozanso kuti mchimwene wake anali atangomwalira kumene ndipo kalata ya Carlee inamuthandiza kuti apilire chisoni chimene anali nacho.

Pomalizira munthuyo ananena kuti: “Usasiye kulembera anthu makalata. Makalata ako amalimbikitsa kwambiri anthu, kaya anthuwo ayankhe makalatawo kapena ayi.”

Panopa Carlee watsimikiza mtima kuti apitirizabe kulembera anthu makalata. Iye ananena kuti, “Ndikusangalala kwambiri kuti Yehova anandigwiritsako ntchito kulimbikitsa munthu wina. Zimene tingalembe m’makalata zikhoza kuwafika pamtima kwambiri anthu.”

Mlongo Myrna Lopez wa ku Center, Texas

Mlongo  Myrna Lopez, yemwe amakhala mu mzinda wa Center ku Texas, anayamba kukayikira ngati makalata ake amathandizadi anthu amene amawalembera. Kenako panachitika zinazake ndi mnyamata wina yemwe anali msuweni wake. Myrna anamva kuti msuweni wakeyo watsekeredwa m’ndende. Choncho iye anaganiza zomulembera kalata. Msuweni wakeyo ali ka mnyamata kakang’ono ankapita nawo ku misonkhano ya Mboni za Yehova ndipo m’kalatayo, Myrna anamutsimikizira kuti Yehova sanamuiwale.

Msuweni wakeyo anayankha kalatayo. Iye anafotokoza kuti anali ndi nkhawa kwambiri atamangidwa ndipo ankaona kuti moyo wake ulibe cholinga. Ali m’ndendemo anayamba kuganizira zimene ankachita ali mwana ndipo anayambiranso kuwerenga Baibulo komanso kupemphera kwa Yehova. Anafotokoza kuti kalata imene Myrna anamulembera inali yankho la pemphero lake komanso umboni woti Yehova amamukondabe.

Mlongo Natalie Bibbs wa ku Norcross, Georgia

Mlongo Natalie Bibbs amakhala mu mzinda wa Norcross, ku Georgia. Iye analandira uthenga wochokera kwa mayi wina amene anapeza imodzi mwa makalata amene analemba. Mayiyo anapeza kalatayo panthawi imene ankathamanga kumalo ena, itaikidwa mphepete mwa msewu. Choyamba mayiyo ataona kalatayo anangoipitirira. Koma kenako pa chifukwa chimene satha kuchifotokoza, anaganiza zobwerera n’kukaitenga.

Mayiyo analembera Natalie kuti: “Mlungu umenewo ndinali nditakumana ndi mavuto ambiri moti ndinkangofuna chinachake chabwino chitandichitikira. Kalata imene ija inali chabwino chomwe ndinkafunikira.”

Natalie anafotokoza kuti: “Zimene mayiyo ananena zinandithandiza kuona kuti Yehova akudalitsa khama lathu, kaya tikugwiritsa ntchito njira ziti zolalikirira.”

Mlongo  Laura Martinez, amakhala mu mzinda wa Athens, ku Texas ndipo amakonda kupereka makalata kwa anthu ogwira ntchito pa golosale ina ya m’dera lawo akamaika zakudya mu galimoto yake. Mayi wina yemwe amagwira ntchito pa golosaleyo anauza Laura kuti kalata yake inamukhudza kwambiri. Kenako Laura analemberanso mayiyo makalata ena awiri ndipo panopa amaphunzira naye Baibulo.

Mlongo Laura Martinez wa ku Athens, Texas, akupereka makalata kwa ogwira ntchito pa golosale ya m’dera la kwawo

Nkhani ngati zimenezi zimatikumbutsa kuti ngakhale kuti sitidziwa pamene mbewu za choonadi “zidzachite bwino,” Yehova akhoza kugwiritsa ntchito mtundu uliwonse wa ulaliki kuti alimbikitse komanso kuthandiza anthu omwe ali ngati nkhosa kukhala ndi chiyembekezo.—Mlaliki 11:6.