JULY 15, 2019
UNITED STATES
Zivomezi Zamphamvu Zagwedeza Kum’mwera kwa California
Kuyambira pa 4 July, 2019, zivomezi zamphamvu komanso zina zing’onozing’ono zakhala zikuchitika kum’mwera kwa California m’dera lachipululu cha Mojave. Chivomezi china chinali champhamvu kwambiri moti m’zaka 20 zapitazi m’derali simunachitikepo chivomezi champhamvu kwambiri ngati chimenechi.
Zivomezizi zinachitika pafupi ndi mzinda wa Ridgecrest, ndipo ofalitsa 215 amakhala mumzindawu. N’zosangalatsa kuti palibe aliyense wa abale athu amene anavulala modetsa nkhawa. Komabe, ofalitsa atatu anavulala pang’ono, komanso malipoti oyambirira akusonyeza kuti ofalitsa 7 anasamuka m’nyumba zawo. Komanso nyumba 7 za abale athu zinaonongeka kwambiri ndipo zina 35 zinaonongeka pang’ono. Kuwonjezera pamenepo, Nyumba za Ufumu ziwiri zinaonongeka pang’ono.
Oyang’anira madera awiri akutsogolera pa ntchito yopereka chithandizo m’derali. Oyang’anira madera komanso akulu a m’derali akulimbikitsa ndiponso kutonthoza abale ndi alongo amene akhudzidwa ndi zivomezizi.
Tikupemphera kuti Yehova apitirize kupereka nzeru kwa abale ndi alongo athuwa kuti athe kupirira ngozi zadzidzidzi ngati zimenezi.—Miyambo 2:6-8.