MAY 29, 2019
UNITED STATES
Zokhudza Misonkhano ya Mayiko ya 2019 Yakuti “Chikondi Sichitha”
Atlanta, Georgia, United States
Madeti: 17 mpaka 19 May, 2019
Malo: Mercedes-Benz Stadium ku Atlanta, Georgia, United States
Zinenero: Chiamuhariki, Chingelezi, Chirasha
Chiwerengero cha Osonkhana: 46,374
Chiwerengero cha Obatizidwa: 314
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,000
Nthambi Zoitanidwa: Australasia, Brazil, Britain, Canada, Chile, Colombia, Ethiopia, Finland, France, Greece, Hong Kong, Israel, Italy, Japan, Kazakhstan, the Netherlands, Portugal, Romania, Scandinavia, Trinidad ndi Tobago
Iyi ndi mbali yoyamba ya zinthu zokhudza misonkhano ya mayiko 24 komanso zithunzi zomwe ziziikidwa pa gawo la Nkhani pa jw.org pambuyo pa msonkhano wa mayiko uliwonse womwe wachitika mu 2019.
Gulu la abale ndi alongo likujambulitsa panja pa malo a msonkhano
M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Loweruka
Abale akubatiza anthu mu limodzi mwa madamu aubatizo awiri omwe anagwiritsidwa ntchito pamsonkhanowu
Abale ndi alongo akumvetsera msonkhano
Ena mwa alendo 164 omwe ali muutumiki wa nthawi zonse wapadera akuyenda mkati mwa sitediyamu ya Mercedes-Benz pa zochitika zomaliza za msonkhanowu pa tsiku Lamlungu
Alendo ochokera kumayiko ena ali muutumiki limodzi ndi abale ndi alongo a ku Georgia
Alendo ochokera kumayiko ena akujambulitsa atavala zovala za kwawo
Ana a Mboni anyamula chinsalu chomwe chili ndi uthenga wopita kwa alendo, wakuti: “Dziko Latsopano Lili Pafupi Kwambiri. Tidzaonana M’Paradaiso”
Alendo ochokera ku Ethiopia avala zovala zachikhalidwe patsiku lomaliza la msonkhano
Gulu la abale ndi alongo omwe amachita zinthu zosiyanasiyana zosangalatsa akubayibitsa anthu omwe amaonerera ndipo kumbuyo kwawo kuli mawu oti “Timakukondani!”