MAY 31, 2019
UNITED STATES
Zokhudza Misonkhano ya Mayiko ya 2019 Yakuti “Chikondi Sichitha”
Miami, Florida (Chisipanishi), United States
Masiku: 24 mpaka 26 May, 2019
Malo: Marlins Park ku Miami, Florida, United States
Chinenero: Chisipanishi
Chiwerengero cha Osonkhana: 28,562
Chiwerengero cha Obatizidwa: 230
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 4,600
Nthambi Zoitanidwa: Argentina, Bolivia, Brazil, Britain, Canada, Central America, Central Europe, Chile, Colombia, Cuba, Ecuador, Paraguay, Peru, Philippines, ndi Spain
Abale ndi alongo a ku Florida akulandira alendo omwe abwera ku Miami
Ana a Mboni atatu akujambulitsa chithunzi pafelemu panja pa malo omwe kunachitikira msonkhanowu
M’bale Kenneth Cook wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Loweruka
Anthu 4 akubatizidwa
Abale ndi alongo akuimba nyimbo pa nthawi ya msonkhano pa tsiku Loweruka
Mlongo wa ku Florida ali limodzi ndi mlendo ndipo akulalikira m’malo opezeka anthu ambiri panja pa Kislak Center, ku koleji ya Miami Dade
Abale ndi alongo omwe ali muutumiki wa nthawi zonse wapadera aima m’bwalo la malo amsonkhano pa nthawi ya nkhani yomaliza pa tsiku Lamlungu
Alongo akukonzekera kugawa zakudya zotchedwa chorizo, empanadas, komanso paella pa nthawi yochereza alendo
Alongo a ku Florida akuvina gule wachikhalidwe cha ku Spain pa nthawi yomwe anthu anakumana pamodzi madzulo
Alendo ochokera kumayiko ena akusangalala ndi zochitika zosiyanasiyana ku malo a msonkhano ku West Palm Beach