JULY 19, 2019
UNITED STATES
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Houston, United States (Chingelezi)
Masiku: 12 mpaka 14 July, 2019
Malo: NRG Stadium ku Houston, Texas, United States
Zinenero: Chingelezi, Chikoleya
Chiwerengero cha Osonkhana: 50,901
Chiwerengero cha Obatizidwa: 401
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,000
Nthambi Zoitanidwa: Australasia, Belgium, Brazil, Britain, Canada, Colombia, Czech-Slovak, France, India, Italy, Japan, Korea, Philippines, ndi Scandinavia
Zina Zomwe Zinachitika: A Sylvester Turner, omwe ndi meya wa mzinda wa Houston, anachita chidwi kwambiri ndi a Mboni za Yehova 50,000 pamodzi ndi alendo awo omwe anabwera kumsonkhano wa ku Houston. Iwo anati: “Tinasangalala kwambiri kulandira a Mboni kuno ku Houston. Zinali ngati tatsegula mawindo kuti mpweya wabwino ulowe. Ngati [a Mboni za Yehova] mungamabwere kawiri pachaka, ndinu olandiridwa mumzinda uno wa Houston. Mudzabwerenso chaka chamawa, komanso chaka chinacho.”
Abale ndi alongo akulandira alendo ku Houston
Alendo akulalikira limodzi ndi abale ndi alongo a ku Houston
Ena mwa abale ndi alongo athu 401 atsopano akubatizidwa
M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Loweruka
Alendo ochokera ku mayiko ena akujambulitsa, ndipo ena avala zovala zakwawo
Alendo akusangalala kukhala limodzi
Abale ndi alongo omwe ali muutumiki wanthawi zonse wapadera akusangalala pamene anthu akuwaombera m’manja pamapeto pa msonkhanowu pa tsiku Lamlungu
Abale ndi alongo a ku Houston ali papulatifomu pambuyo pa zochitika zosiyanasiyana zamadzulo monga kuimba, kuvina, komanso kufotokoza mwachidule zokhudza mbiri ya Mboni za Yehova ku Houston