AUGUST 29, 2019
UNITED STATES
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Houston, United States (Chisipanishi)
Masiku: 23 mpaka 25 August, 2019
Malo: NRG Stadium ku Houston, Texas, United States
Chinenero: Chisipanishi
Chiwerengero cha Osonkhana: 56,167
Chiwerengero cha Obatizidwa: 626
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,500
Nthambi Zoitanidwa: Argentina, Bolivia, Central America, Chile, Colombia, Dominican Republic, Ecuador, France, Italy, Japan, Peru, Philippines, Spain, Trinidad ndi Tobago, komanso Venezuela
Zina Zomwe Zinachitika: A Joelle Hardin omwe ndi mkulu woona zamalonda komanso kusungira malo makasitomala ku Space Center Houston anati: “M’mawawu mmodzi mwa anthu omwe ndimagwira nawo ntchito [yemwe ankachita sikani matikiti pamene alendo ankalowa] anabwera kwa ine n’kunena kuti: ‘Joelle, . . . aliyense amandiyang’ana n’kundiuza kuti, “Zikomo,” ndipo ena amandiuza zimenezi m’zinenero zina.’ Zimenezi zinachititsa kuti akhale wosangalala tsiku lonse. N’kale limene ndinamuona atasangalala kwambiri choncho.”
Alendo akufika pasitediyamu m’mawa
Alendo akulalikira limodzi ndi abale ndi alongo a ku Texas
Abale ndi alongo ambiri ongodzipereka akuyeretsa sitediyamu ya NRG Stadium Lachisanu msonkhano usanayambe
Awiri mwa abale ndi alongo 626 atsopano akubatizidwa
M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza Lachisanu masana
Alendo akulemba notsi uku akumvetsera nkhani pa msonkhanowu
Mlongo akuonetsa alendo malo osungirako zinthu zakale a Houston Museum of Natural Science, pa ulendo wina wokaona malo womwe alendowa anapita
Abale ndi alongo athu akuvina pa zochitika zina zamadzulo
Abale ndi alongo omwe ali muutumiki wanthawi zonse wapadera ali m’bwalo la sitediyamu ndipo akubayibitsa pojambulitsa Lamlungu msonkhanowu utatha