JULY 12, 2019
UNITED STATES
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Miami, United States (Chingelezi)
Masiku: 5 mpaka 7 July, 2019
Malo: Marlins Park ku Miami, Florida, United States
Zinenero: Chingelezi, Chitchainizi cha Chimandarini
Chiwerengero cha Osonkhana: 28,000
Chiwerengero cha Obatizidwa: 181
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,000
Nthambi Zoitanidwa: Australasia, Brazil, Britain, Canada, Colombia, Dominican Republic, Fiji, Ghana, Greece, Hong Kong, Israel, Japan, Netherlands, Scandinavia, South Africa, Spain, Taiwan, Trinidad ndi Tobago, Ukraine
Zina Zomwe Zinachitika: Lamlungu, a Francis X. Suarez, omwe ndi meya wa mzinda wa Miami, anapita kumsonkhanowu ndipo anati: “Zandisangalatsa kuti uthenga womwe ukunenedwa pamsonkhanowu ndi wakuti ‘Chikondi Sichitha.’ Uthenga umenewu ndi wolimbikitsa kwabasi.” Iwo ananenanso kuti: “Ndikuona kuti [msonkhanowu] ndi wofunika kuti uzichitika m’mizinda ikuluikulu ku United States kuno kapenanso padziko lonse.”
Achinyamata ali m’gulu la anthu omwe akulandira alendo pabwalo la ndege la Miami International Airport
Alendo ochokera kumayiko ena akugwira ntchito yoitanira anthu ku msonkhano limodzi ndi a Mboni a ku Miami
Alendo akulandira Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso la Chitchainizi lomwe linatulutsidwa pa tsiku Lachisanu
Alendo akulemba manotsi pamene akumvetsera msonkhanowu
Atatu mwa abale ndi alongo 181 atsopano akubatizidwa
Abale ndi alongo a ku Miami akupereka moni kwa alendo komanso akupatsana mphatso
Amishonale ndi atumiki a pa Beteli omwe akutumikira m’mayiko ena akubayibitsa anthu masauzande ambiri pabwalo la sitediyamu pa tsiku Lamlungu masana
Lamlungu pambuyo pamsonkhano, M’bale Lösch akupereka moni kwa omwe ali mu utumiki wanthawi zonse wapadera
Ana akuimba nyimbo zosangalatsa alendo pa zochitika zapadera madzulo