AUGUST 15, 2019
UNITED STATES
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Phoenix, United States
Masiku: 9 mpaka 11 August, 2019
Malo: Chase Field ku Phoenix, Arizona, United States
Chinenero: Chingelezi
Chiwerengero cha Osonkhana: 40,237
Chiwerengero cha Obatizidwa: 352
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,000
Nthambi Zoitanidwa: Australasia, Britain, Canada, Central Europe, Chile, France, Greece, India, Italy, Korea, Micronesia, Scandinavia, Sri Lanka, Tahiti, Thailand, Trinidad and Tobago, ndi Turkey
Zina Zomwe Zinachitika: A Steve Moore, omwe ndi pulezidenti ndiponso mkulu wa kampani ya Visit Phoenix yomwe imathandiza anthu kupeza malo ochitira misonkhano, mahotela komanso kokachitira holide m’dera la Phoenix, anati: “Ndakhala ndikugwira ntchitoyi kwa nthawi yayitali, ndipo [msonkhanowu] ndi umene wakonzedwa bwino kwambiri pa misonkhano yonse imene ndakhala ndi mwayi wogwira nawo ntchito. Kuonjezera pamenepo, mwalonjeza kuti muyeretsa sitediyamuyi musanapite, palibe amene amachita zimenezi.”
Alendo akulandiridwa ndi manja awiri pamene akufika pabwalo la ndege la Sky Harbor International Airport ku Phoenix
Abale ndi alongo a ku Phoenix akonzekera kuti alandire alendo ku imodzi mwa mahotela omwe alendowo anafikira
Abale ndi alongo mahandiredi ambiri akupereka moni mosangalala kwa alendo pamene akufika pa Chase Field Lachisanu m’mawa
Alendo akumvetsera msonkhano ndipo ena avala zovala za kwawo
Awiri mwa abale ndi alongo 352 atsopano akubatizidwa
M’bale Samuel Herd wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku lachiwiri la msonkhanowu
Alendo akudzijambula pamene akuona malo ku nkhalango ya boma
Abale athu akwera ngolo yokokedwa ndi mahatchi ngati mbali yosonyeza mbiri ya tauni ina ya m’zaka za 1800 ku American West
Atumiki a nthawi zonse ochokera kumayiko ena ali m’bwalo la sitediyamu pamapeto pa msonkhano pa tsiku Lamlungu