AUGUST 23, 2019
UNITED STATES
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku St. Louis, United States
Masiku: 16 mpaka 18 August, 2019
Malo: The Dome at America’s Center ku St. Louis, Missouri, United States
Zinenero: Chingelezi ndi Chikolowesha
Chiwerengero cha Osonkhana: 28,122
Chiwerengero cha Obatizidwa: 224
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,000
Nthambi Zoitanidwa: Argentina, Australasia, Britain, Canada, Central Europe, Colombia, Croatia, Czech-Slovak, Finland, France, Japan, Philippines, Poland, Portugal, Scandinavia, Serbia, ndi South Africa
Zina Zomwe Zinachitika: A Martin Gulley omwe amalankhula m’malo mwa kampani ya Metrolink, anati: “Munthu ukhoza kunena kuti umakonda winawake. Ukhozanso kunena kuti umakonda chinachake. Koma sitinganene kuti ndi chikondi chenicheni ngati munthu sakuchita zinthu zosonyeza chikondicho. Inu a Mboni mukuchita zinthu zosonyeza chikondi. Ndinu anthu odzichepetsa, ndipo chikondi chimachititsa anthu kukhala odzichepetsa, osati kukhala odzikuza. Anthu amandidziwa kuti ndimagwira ntchito ku Metrolink chifukwa cha baji imene ndimavalayi. Koma inuyo mumadziwika kuti ndinu a Mboni za Yehova chifukwa cha chikondi.”
A Jerry Vallely, omwe amalankhula m’malo mwa kampani ya Bi-State Development (yomwe imapititsa patsogolo nkhani za chuma m’chigawo cha St. Louis), anaonjezera kuti: “Sikuti mumangoganizira za ntchito zomwe zifunika kugwiridwa. Koma mumaganizira za anthu omwe apindule ndi ntchitozo, kaya ndi alendo omwe akubwera kumsonkhanowu, ogwira ntchito mumzindawu omwe mukugwira nawo ntchito limodzi, kapenanso ifeyo kuno ku Metrolink. Mumaganizira za aliyense amene mukugwira naye ntchito ndipo mumachita zomwe mungathe kuti zinthu ziyende bwino.”
Abale ndi alongo a ku St. Louis akudikirira kuti alendo omwe akubwera kumsonkhanowu afike pa bwalo la ndege la St. Louis Lambert International Airport
Alendo akulalikira ndi abale ndi alongo a ku St. Louis pogwiritsa ntchito mashelefu m’tawuni ya St. Louis
Abale ndi alongo akuyeretsa malo a msonkhano omwe amadziwika kuti “The Dome,” msonkhano usanayambe
Atatu mwa abale ndi alongo 224 atsopano akubatizidwa
M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku lachitatu la msonkhanowu
Alendo akumwetulira pamene akumvetsera msonkhano
Abale ndi alongo ochokera kumayiko ena omwe akuchita utumiki wa nthawi zonse wapadera akubayibitsa anthu m’bwalo la sitediyamu pa tsiku Lamlungu
Alendo akujambulitsa limodzi ndi abale ndi alongo a ku St. Louis
Alendo akusangalala kuona nyama kumalo oonetserako zinyama a Saint Louis Zoo
Alendo akuona Baibulo loyamba la mu 1611 la King James Version lomwe silipezekapezeka. Baibuloli lili mu laibulale ya St. Louis Public Library ndipo latsegulidwa pa lemba la Salimo 83:18. Ogwira ntchito mulaibulaleyi anakonza zoti Baibuloli litsegulidwe patsamba lomwe pali lembali chifukwa cha alendowa
Abale ndi alongo achinyamata akuimba pa zochitika zamadzulo