Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JANUARY 13, 2020
UNITED STATES

Zomwe Zachitika pa Ntchito Yothandiza Anthu Omwe Anakhudzidwa ndi Mphepo Yamkuntho ya Dorian

Thandizo Linafika pa Ndege ndi pa Maboti

Zomwe Zachitika pa Ntchito Yothandiza Anthu Omwe Anakhudzidwa ndi Mphepo Yamkuntho ya Dorian

Mphepo yamkuntho ya Dorian inawononga ku Bahamas pa 1 mpaka pa 3 September, 2019. Mphepoyi isanawombe, ofesi ya nthambi ya United States inayamba kukonzekera ntchito yopereka chithandizo kuchokera ku Florida, U.S.A. Atamaliza zonse zokonzekera, abale omwe ali ndi maboti komanso ena omwe ali ndi ndege, ananyamuka ulendo wopita ku zilumbazi ndipo anali oyambirira kugwira ntchito yopereka chithandizo kumeneko.

Abale ndi alongo 13 anayenda pandege kwa maulendo oposa 300 atatenga zinthu zosiyanasiyana zolemera matani 15 komanso anatenga abale ndi alongo ongodzipereka 700 n’kuwapititsa m’madera omwe anakhudzidwa ndi mphepo yamkunthoyi. Kuwonjezera pamenepa, abalewa ananyamula zinthu zolemera matani pafupifupi 90 pogwiritsa ntchito maboti awo 13. Pa avereji, ulendo wa pamaboti unatenga maola 12 kuchokera ku Florida kupita ku Bahamasi ndi kubwerera.

A Jose Cabrera omwe amayang’anira za maulendo a pandege ku Palm Beach International Airport m’dziko la Florida, anati: “Mphepo yamkunthoyi itangochitika, ndege [za a Mboni] zinanyamuka kupita ku Bahamas zitatenga zinthu zosiyanasiyana pokathandiza anthu. A Mboni ndi anthu achitsanzo chabwino kwambiri ndipo anachita zinthu zoposa zimene timayembekezera.”

M’bale Glenn Sanders yemwe ndi mmodzi mwa abale ndi alongo omwe anadzipereka kuyendetsa ndege anati: “Ambiri mwa ife kanali koyamba kugwiritsa ntchito luso lathu loyendetsa ndege pa ntchito yothandiza abale ndi alongo athu. Zinali zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti tinali ngati chiwalo chaching’ono cha thupi chomwe chikugwira ntchito yothandiza chiwalo china cha thupi chimene chikuvutika.”—1 Akorinto 12:26.

Ofesi ya nthambi ya United States yanena kuti ntchito yopereka chithandizoyi idzafunika ndalama pafupifupi madola 1,750,000 a ku America ndipo ntchitoyi idzakhala itatha pofika pa 1 May, 2020.

 

Akulongedza katundu wosiyanasiyana pamalo omwe amalongedzera zinthu m’maboti ku Florida, U.S.A. Abale athu anayenda pamaboti maulendo 29 kupita ku Bahamas

Bwalo la ndege lomwe linasefukira ndi madzi ku Great Abaco, Bahamas

Akuyendetsa ndege