Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 6, 2016
UNITED STATES

A Mboni za Yehova Agulitsa Nyumba Imene Akhala Akugwiritsa Ntchito kwa Zaka Zambiri M’dera Lotchuka la Brooklyn Heights

A Mboni za Yehova Agulitsa Nyumba Imene Akhala Akugwiritsa Ntchito kwa Zaka Zambiri M’dera Lotchuka la Brooklyn Heights

NEW YORK—Lachiwiri pa 26 April, 2016, a Mboni za Yehova anamaliza ntchito yogulitsa nyumba yawo ya 124 Columbia Heights ku New York. Nyumbayi, yomwe kukula kwake ndi mamita 14,121 mbali zonse ndipo ili ndi chikwangwani cha Watchtower padenga lake, ili cha kumpoto kwa msewu womwe wadutsa m’mphepete mwa mtsinje ku Brooklyn Heights. Mu December 2015 ndi pamene anthu anayamba kunena kuchuluka kwa ndalama zimene angapereke kuti agule nyumbayi. Pambuyo pake, munthu woti agule nyumbayo anasankhidwa ndipo anali woyamba kugula imodzi mwa nyumba zimene a Mboni akugulitsa.

Mmene nyumba ya 122-124 Columbia Heights inkaonekera a Mboni za Yehova asanaikonze.

Nyumbayi yomwe poyamba inali ndi nsanjika 4 ndipo ndi yofiirira, inali ya bambo Henry Ward Beecher omwe anali odziwika bwino pa nkhani yolimbana ndi zinthu zimene ankaziona kuti ndi zolakwika. Iwo analinso m’busa wa tchalitchi cha Plymouth kuyambira mu 1856 mpaka 1881. Nyuzipepala ya The New York Times inalemba nkhani yofotokoza mbiri ya nyumba imeneyi, ndipo inanena kuti “munali m’nyumba imeneyi mmene a Abraham Lincol, omwe anali mtsogoleri wa dziko la America, anakakumana ndi a Beecher atatsala pang’ono kusainira lamulo lothetsa ukapolo.” Mu May 1909, a Mboni za Yehova anagula nyumbayi ndipo kenako anagulanso nyumba zina zoyandikana nayo ndipo panopa nyumbayi ili ndi nsanjika 10.

Bambo Richard Devine omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ananena kuti: “Nyumba ya 124 Columbia Heights ndi imodzi mwa nyumba zimene gulu lathu lakhala likugwiritsa ntchito kwa zaka zambiri. Kuyambira mu 1909, nyumbayi kwenikweni yakhala ikugwiritsidwa ntchito monga nyumba yokhalamo anthu amene amagwira ntchito pa likulu lathu. Kuyambira mu 1929 mpaka 1957, kupatulapo zaka 4 zokha, m’nyumbayi munalinso siteshoni ya wailesi yathu yotchedwa WBBR imene ankaulutsirapo nkhani za m’Baibulo komanso mapulogalamu ena ofotokoza Baibulo.”

Situdiyo ya wailesi ya Mboni za Yehova yotchedwa WBBR ku 124 Columbia Heights m’zaka za m’ma1950.

Ngakhale kuti a Mboni za Yehova akhala ku Brooklyn Heights kwa zaka zoposa 100, likulu la bungwe lawo la Watch Tower Bible and Tract Society linakhazikitsidwa m’zaka za m’ma 1880 ku Allegheny, komwe panopa ndi mbali ya Pittsburgh ku Pennsylvania. Bambo David A. Semonian, omwe amayankhula m’malo mwa a Mboni ku likululi ananena kuti: “Kusamukira mu mzinda wa Brooklyn womwe uli ndi doko kumene kunachitika mu 1909, kunali kofunika kwambiri pa nthawiyo ndi cholinga chopititsa patsogolo ntchito yathu yophunzitsa anthu Baibulo yomwe ikuchitika pa dziko lonse.”

Kugulitsa nyumba ya 124 Columbia Heights ndi chinthu chimene a Mboni achita posachedwapa pamene akusamutsira ma ofesi a likulu lawo ku Warwick, New York. Ma ofesi atsopanowa ali pa malo omwe kukula kwake ndi pafupifupi maekala 50 ndipo ntchito yamanga malowa ikuyembekezeka kutha posachedwapa. A Semonian ananenanso kuti: “Kusamukira ku malo athu atsopanowa, amene amangidwa mogwirizana ndi zimene timafuna pa ntchito yathu, ndi chinthu chimene tikufunikadi kuchita panopa. Ku Brooklyn takhalako kwa zaka zoposa 100 ndipo ku Warwick ndi kumene tsopano kukhale likulu lathu.”

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000