Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 6, 2018
UNITED STATES

Ku Alaska Kwachitika Chivomezi Champhamvu Kwambiri

Ku Alaska Kwachitika Chivomezi Champhamvu Kwambiri

Pa 30 November, 2018, chivomezi champhamvu kwambiri chinachitika pafupi ndi mzinda wa Anchorage ku Alaska. Ofalitsa nkhani ananena kuti chivomezichi chinawononga kwambiri misewu ngakhale kuti palibe munthu yemwe anavulala kwambiri kapena kuphedwa.

Ofesi ya nthambi ku United States inanena kuti ofalitsa 7 anavulala pang’ono chifukwa cha chivomezichi. Nyumba 16 za abale athu ndiponso Nyumba za Ufumu ziwiri zinaonongeka. Mogwirizana ndi malangizo ochokera kwa oyang’anira madera, mipingo ikupereka chakudya, zovala, madzi komanso malo okhala kwa anthu amene anakhudzidwa ndi chivomezichi. Akulu nawonso akugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo potonthoza onse amene anakhudzidwa.

Tipitirizabe kupempherera abale athu amene anakhudzidwa ndi chivomezichi. Tikukhulupirira kuti Yehova awapatsa mphamvu komanso akhala malo achitetezo kwa anthu ake pamene akupitirizabe kumudalira.—Salimo 28:8, 9.