DECEMBER 7, 2015
UNITED STATES
A Mboni Ayamba Kugulitsa Nyumba Zawo za ku Brooklyn
NEW YORK—A Mboni za Yehova akugulitsa nyumba zawo zomwe anthu ambiri akhala akuzifuna ndipo nyumbazi zili m’dera la Dumbo ndiponso Brooklyn Heights mumzinda wa New York. Panopa akugulitsa malo a ku 85 Jay Street ku Brooklyn komanso nyumba yansanjika 10 ku 124 Columbia Heights. A Mboniwa akugulitsanso nyumba zawo zomwe zili kulikulu lawo ku 25/30 Columbia Heights. Ofesi ya a Mboniwa yoona zogulitsa malo ndi imene ikugwira ntchito yogulitsa malo ndiponso nyumba ziwirizi.
A Richard Devine, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova, alankhulapo zokhudza kugulitsa malo a ku Jay Street ndipo anena kuti: “Malowa ndi aakulu kwambiri ndipo ali m’dera losiririka la Dumbo. Komanso chilolezo chilipo kale kuti munthu amange nyumba pa masikweya mita 92,903 a malowa.”
Nyumba ya a Mboni yomwe ili ku 124 Columbia Heights, ili m’mbali mwa mtsinje kumalo abwino zedi a ku Brooklyn. A Devine ananenanso kuti: “Nyumbayi ili pamalo abwino kwambiri moti anthu amaona mosavuta zinthu monga mlatho wa Brooklyn, chipilala chachikumbutso chodziwika kwambiri komanso nyumba zazitali kwambiri za m’dera la Manhattan .”
Likulu la Mboni za Yehova ku 25/30 Columbia Heights (chithunzi chomwe chili pamwambapa) lakhala kumalowa kwa zaka zambiri moti anthu ambiri a m’derali akulidziwa chifukwa cha chikwangwani chodziwika bwino cha Watchtower. Likululi ndi lalikulu masikweya mita 68,098 ndipo anthu akakhala pamalowa amaona mosavuta mlatho wa Brooklyn.
Pofotokoza zokhudza kugulitsa nyumbazi, a Divine ananenanso kuti: “Kugulitsa nyumbazi kukusonyeza kuti posachedwapa tisamukira kulikulu lathu latsopano ku Warwick, New York.”
Kuti mudziwe zambiri zokhudza nyumbazi, mukhoza kutsegula linki iyi www.watchtowerbrooklynrealestate.com. Zithunzi za nyumbazi komanso zinthu zina zokhudza kugulitsa nyumbazi mungazidziwe kudzera ku Ofesi Yofalitsa Nkhani.
Lankhulani ndi:
David A. Semonian, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000