31 OCTOBER, 2017
UNITED STATES
Vidiyo ya Mboni Yathandiza Makolo Kudziwa Zimene Angachite Kuti Athandize Ana Amene Amavutitsidwa ndi Anzawo
NEW YORK—Pakafukufuku yemwe anachitika ndi chipatala china cha ana mu 2017 (C.S. Mott Children’s Hospital National Poll on Children’s Health), panapezeka kuti makolo ambiri ku United States akudandaula kuti kuzunzidwa ndi vuto lomwe limakhudza kwambiri thanzi la ana awo. Kafukufukuyu anachitikira pa yunivesite ya Michigan.
Webusayiti ina yotchedwa stopbullying.gov, yomwe imayang’aniridwa ndi dipatimenti ya zaumoyo ndi kusamalira anthu (U.S. Department of Health & Human Services), inanena chifukwa china chimene chimachititsa kuti makolo azidera nkhawa. Webusaitiyi inanena kuti malinga ndi kafukufuku wina, ana asukulu 30 pa 100 aliwonse ku U. S. amazunzidwa ndi anzawo kusukulu.
A David A. Semonian, omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku likulu lawo lapadziko lonse ku New York, ananena kuti: “Timadziwa kuti kuzunzidwa ndi vuto lalikulu limene limadetsa nkhawa ana ambiri. Choncho, monga mbali ya ntchito yathu yophunzitsa anthu Baibulo, timayesetsa kukonza mabuku ndi mavidiyo omwe amafotokoza zokhudza kuzunzidwa ndiponso mavuto ena amene mabanja akukumana nawo. Kwa zaka pafupifupi 5 tsopano, mabanja ambiri padziko lonse athandizidwa kwambiri ndi vidiyo yathu ya makatuni ya mutu wakuti Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani?”
Vidiyoyi ndi ya maminitsi osapitirira 4, ndipo ikupezeka pawebusaiti ya jw.org m’zilankhulo zoposa 280 komanso m’zinenero zamanja zoposa 30.
Natalia Cárdenas Zuluaga, yemwe ndi mkulu woyang’anira pulogalamu ina (Child and Adolescent Mental Health) pa yunivesite ya CES ku Colombia anati: “Ndikuona kuti mfundo zimene zafotokozedwa mu vidiyoyi n’zothandiza kwambiri chifukwa m’dziko lathu lino, nthawi zina makolo amaphunzitsa ana awo kuti azibwezera anzawo akawaputa. Ndikuganiza kuti vidiyo imeneyi ili ndi mfundo zothandiza kwambiri kwa ana amene akuvutitsidwa. Imafotokozanso mfundo yofunika kwambiri yokhudza kuvutitsidwa yakuti: Munthu amatha kuvutitsidwa chifukwa choti ndi wosiyana ndi anzake. Ana akadziwa mfundo imeneyi amatha kuugwira mtima komanso amadziona kuti nawonso ndi ofunika.”
Pulofesa wina wa pa yunivesite ya Sungkyunkwan ku South Korea, dzina lake Dr. Jun Sung Hong, ananena kuti: “Popeza kuti vidiyoyi ndi yamakatuni, imakopa chidwi ndipo ndi yothandiza kwambiri kwa ana, makamaka amene akuvutitsidwa. Ndikuonanso kuti munthu akaionera, sangavutike kukumbukira zomwe waonazo chifukwa choti ili ndi zithunzi zamakatuni.”
Kuonjezera pamenepo, a Dr. Shelley Hymel omwe anayambitsa nawo ntchito yofufuza nkhani zokhudza kuvutitsidwa m’mayiko osiyanasiyana anati: “Ndikuganiza kuti vidiyoyi ili ndi uthenga wothandiza kwa ana ndipo ikugwirizana ndi kafukufuku amene ndimapanga. Ndi yothandiza kwambiri kwa makolo, aphunzitsi kapena anthu ena amene amagwira ntchito zokhudza ana komanso achinyamata. Ndipo makolo, aphunzitsi kapena anthu ena amene amagwira ntchito zokhudza ana komanso achinyamata sangavutike kuigwiritsa ntchito pothandiza ana.”
A Semonian ananenanso kuti: “Timadera nkhawa ana amene amavutitsidwa ndipo tikukhulupirira kuti malangizo amene ali m’vidiyoyi awathandiza. Monga mmene vidiyoyi ikufotokozera, ana amene amavutitsidwa ayenera kufotokozera munthu wodalirika, makamaka makolo kapena aphunzitsi awo amene angawapatse malangizo othandiza. Iwo sayenera kulimbana ndi vuto limeneli paokha.”
Lankhulani ndi:
David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000