Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 15, 2018
UNITED STATES

Moto Wolusa Wawononga Kwambiri ku California

Moto Wolusa Wawononga Kwambiri ku California

Zomwe Zangochitika Kumene: Ofesi ya Nthambi ya ku United States yatsimikizira kuti m’bale wazaka 70 wa ku Paradise, Kumpoto kwa California, wafa chifukwa cha moto wolusa wotchedwa Camp Fire.

Moto wolusa kwambiri wotchedwa Camp Fire, Hill Fire ndi Woolsey Fire wawononga kwambiri ku California m’dziko la United States ndipo anthu osachepera 48 afa. Moto woopsa kwambiri wotchedwa Camp Fire ukupitirizabe kuyaka Kumpoto kwa California ndipo wawononga kale dera lokwana maekala 117,000 komanso wawononga nyumba pafupifupi 7,100 ndipo zambiri ndi nyumba zokhalamo. Kum’mwera kwa California, moto wotchedwa Hill Fire ndi Woolsey Fire, wawononga dera lokwana maekala 94,500 ndiponso nyumba pafupifupi 435. Lipoti lina la ofalitsa nkhani lanena kuti moto umene wabuka ku California chaka chino “wawononga dera lalikulu kuposa dziko la Belgium ndi dziko la Luxembourg.”

Malipoti ochokera ku ofesi ya nthambi ya United States akusonyeza kuti moto wa Camp Fire unachititsa kuti ofalitsa pafupifupi 427 mumzinda wa Chico ndi m’tawuni ya Paradise athawe m’nyumba zawo. N’zomvetsa chisoni kuti mlongo wina wachikulire wa mumpingo wa Ponderosa anafa chifukwa cha moto wolusawu. Komanso panopa zatsimikizika kuti nyumba za abale athu zosachepera 94 zinawonongeka ndipo zina mwa zimenezi zinawonongeka kwambiri. Nyumba ya Ufumu imodzi ku Paradise yawonongekanso.

Moto wa Hill ndi wa Woolsey unachititsa kuti ofalitsa 420 a m’mizinda ya Oxnard, Simi Valley, komanso Thousand Oaks athawe m’nyumba zawo. N’zomvetsa chisoni kuti m’bale wina limodzi ndi mayi ake omwe si Mboni anafa pamene ankathawa motowu ku Malibu. Malipoti oyambirira akusonyeza kuti nyumba 21 za abale athu ndi Nyumba ya Ufumu imodzi zawonongeka.

Ofesi ya nthambi yakhazikitsa makomiti awiri othandiza pangozi zadzidzidzi kuti agwire ntchito yothandiza abale athu. Oyang’anira madera anapempha akulu kuti azilimbikitsa ndi kutonthoza ofalitsa amene anakhudzidwa ndi motowu. Loweruka pa 10 November abale ndi alongo a ku Chico anapezeka pa msonkhano wapadera. Pamsonkhano wapaderawu, m’bale wa mu Komiti ya Nthambi ya United States limodzinso ndi oyang’anira madera anakamba nkhani zolimbikitsa.

Ndi pemphero lathu kuti Yehova alimbikitse komanso kutonthoza abale ndi alongo omwe akuvutika chifukwa cha moto wolusawu ndipo nthawi zonse azikumbukira kuti posachedwapa Yehova adzapukuta misozi yonse ndi kumeza imfa kwamuyaya.—Yesaya 25:8.