Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 15, 2018
UNITED STATES

Chiphala Chotentha Chapansi Panthaka Chawononga Zinthu Komanso Chachititsa Kuti Anthu Asamuke ku Hawaii

Chiphala Chotentha Chapansi Panthaka Chawononga Zinthu Komanso Chachititsa Kuti Anthu Asamuke ku Hawaii

Kuyambira pa 3 May, 2018, chiphala chotentha chapansi panthaka chotchedwa Kilauea chomwe chimaphulikaphulika pachilumba chachikulu kwambiri ku Hawaii, U.S.A., chinachititsa kuti anthu pafupifupi 2,000 omwe ankakhala pachilumbachi asamuke komanso chinawononga nyumba zosachepera 36.

Mabanja 4 a Mboni komanso mlongo m’modzi wachikulire anasamutsidwa pamodzi ndi anthu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi. Ngakhale kuti palibe Nyumba za Ufumu zomwe zaonongeka ndi chiphala chotenthachi, chivomezi champhamvu chinawononga pang’ono Nyumba ya Ufumu ina pa 4 May.

Komiti yothandiza anthu pakachitika ngozi zadzidzidzi ikugwira ntchito limodzi ndi abale ndi alongo a m’deralo pothandiza ofalitsa omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi. Komitiyi iona ngati pangafunikire thandizo loonjezera zinthu zikakhala m’malo.

Chifukwa cha ngoziyi yomwe imachitikachitika, tipitiriza kupempherera abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi ndiponso tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova akhala malo awo achitetezo pa nthawi yovutayi.—Nahumu 1:7.