Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

OCTOBER 26, 2016
UNITED STATES

A Mboni akugulitsa Nyumba Yawo ya ku 97 Columbia Heights

A Mboni akugulitsa Nyumba Yawo ya ku 97 Columbia Heights

Kwa zaka zambiri, Hotel Margaret inali nyumba yayitali kwambiri ku Brooklyn.

NEW YORK—Lachitatu pa 26 October, 2016, a Mboni za Yehova analengeza kuti akugulitsa nyumba yawo ya ku 97 Columbia Heights ku New York. Nyumbayi ndi yokongola kwambiri ndipo kutalika kwake ndi nyumba zosanjikizana 11. Kuchokera pa nyumbayi anthu amatha kuona mtsinje wa East River, nyumba zazitali kwambiri za m’dera la Manhattan komanso malo ena ofunika mu mbiri ya dera la Brooklyn Heights.

97 Columbia Heights inamangidwa potengera pulani ya nyumba yogona yokhala ndi mawindo komanso zinthu zina zofanana ndi hotelo yomwe inapsa.

Nyumbayi ili pomwe panali hotela ina yotchedwa Hotel Margaret yomwe inapsa ndi moto m’chaka cha 1980. Katswiri wa zomangamanga dzina lake Stanton Eckstut anapangidwa hayala kuti alembe pulani ya nyumba yogona yokhala ndi mawindo komanso zinthu zina zofanana ndi hotelo yomwe inapsayo. Koma nyumbayi anaigulitsa kwa a Mboni mu 1986 asanamalize kuimanga ndipo ankaigwiritsa ntchito ngati malo ogona anthu ogwira ntchito kulikulu la Mboni za Yehova. A David A. Semonian omwe amalankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku likulu lawo, ananena kuti: “Kwa zaka 30 zapitazi, anthu ambiri ankangoona nyumba ya ku 97 Columbia Heights ngati kwawo. Ndipo nyumbayi ndi malo abwino ogonamo chifukwa cha pamalo omwe ili komanso ndi yokongola.”

Nyumbayi kukula kwake ndi masikweya mita 8,232 ndipo ili ndi zipinda zogona 97 zomwe zina zili ndi makonde komanso malo ochezera a padenga. Ilinso ndi galaja mkati ndipo ili ndi malo oimika magalimoto 30. Magalimoto amalowa mugalajayi podzera mumsewu wa ku Orange Street.

A Semonian anafotokozanso kuti: “Anthu komanso ma ofesi athu onse asamukira kulikulu lathu latsopano ku Warwick, ku New York ndipo anayamba kugwira ntchito pa 1 September, 2016. Kugulitsa nyumba ya 97 Columbia Heights ndi ndi umboni wina wosonyeza kuti tasamukadi.”

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000