Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 2, 2018
UNITED STATES

Madzi Osefukira Awononga Kuchigawo Chapakati cha United States

Madzi Osefukira Awononga Kuchigawo Chapakati cha United States

M’mwezi wa February 2018, kuchigawo chapakati cha United States kunasefukira madzi omwe anabwera chifukwa cha mvula yamphamvu komanso sinowo yemwe anasungunuka. Abale ndi alongo athu omwe amakhala m’madera a Illinois, Indiana, Kentucky, Michigan, Ohio, ndi Tennessee ali m’gulu la anthu omwe anakhudzidwa ndi kusefukira kwa madziku.

Ofesi ya Nthambi ya ku United States yanena kuti ofalitsa 20 a m’madera 8 asamuka m’nyumba zawo chifukwa chokhudzidwa ndi kusefukira kwa madziku. N’zomvetsa chisoni kuti mlongo wina wa ku Indiana anamwalira pangoziyi. Nyumba za abale zokwana 57 zawonongedwa ndi madzi osefukirawa.

Oyendera madera a m’zigawo zokhudzidwazi akuyesetsa kulimbikitsa abale ndi alongo amene akhudzidwa kwambiri ndi ngoziyi. Nafenso tikupitirizabe kupempherera abale ndi alongo athuwa podziwa kuti Yehova adzawatonthoza.—1 Petulo 5:7.

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000