Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 13, 2015
UNITED STATES

A Mboni za Yehova Atsegulira Ofesi Yomasulira Chinenero Chamanja cha ku America Kudera la Florida

A Mboni za Yehova Atsegulira Ofesi Yomasulira Chinenero Chamanja cha ku America Kudera la Florida

Pa November 14, 2014, a Mboni za Yehova anayamba ntchito yosamutsa gulu la anthu omasulira chinenero chamanja cha ku America kuchoka ku Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson kupita mumzinda wa Fort Lauderdale ku Florida. A Mboniwa akhala akumasulira Baibulo ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo m’chinenero chamanja chimenechi kuyambira mu 1995 kumaofesi awo a ku Patterson. M’miyezi yapitayi, iwo akhala akukonza nyumba yawo ya ku Fort Lauderdale kuti kukhale maofesi ndiponso situdiyo. Maofesiwa anayamba kugwira ntchito mu May 2015.

Mavidiyo a chinenero chamanjachi amapezeka pa webusaiti ya jw.org ndiponso pa ma DVD. Amagwiritsanso ntchito mavidiyowa pamisonkhano yawo mlungu uliwonse m’mipingo yoposa 500 ndiponso pamisonkhano yawo ikuluikulu.

Munthu amene amagwirizanitsa ntchito yomasulira chinenerochi ku Florida dzina lake Jonathan Galvez anati: “Cholinga chathu ndi kuyesetsa kuti mavidiyo athu azikhala omveka bwino kwa anthu amene amagwiritsa ntchito chinenero chamanja cha ku America, kaya amachokera kuti kapena anaphunzira bwanji.” Iye ananenanso kuti: “Pali mayiko pafupifupi 45 amene anthu amagwiritsa ntchito chinenero chamanja cha ku America. Mofanana ndi zinenero zina, anthu amalankhula chinenerochi mosiyanasiyana malinga ndi kumene amakhala. Mumzinda wa Fort Lauderdale muli anthu ochokera mayiko osiyanasiyana omwe amagwiritsa ntchito chinenero chamanja cha ku America. Izi zimathandiza omasulirawo kuti adziwe mmene anthu ambiri amalankhulira chinenerochi.”

Mu 2014, katswiri wina wa zinenero dzina lake Frank Bechter anapita kumsonkhano waukulu wa Mboni za Yehova wa m’chinenero chamanja cha ku America, umene unachitikira mumzinda wa Richmond ku Virginia. Anapezeka pamsonkhanowu chifukwa chofuna kuchita kafukufuku wokhudza chinenero chamanja ndiponso anthu amene ali ndi vuto losamva. Iye anati: “Pamsonkhanowu, zinaonekeratu kuti gulu lanu limayesetsa kumasulira ndiponso kugwiritsa ntchito bwino chinenero chamanja cha ku America. Chinenero chamanja cha m’mavidiyo anu omasulira mavesi a m’Baibulo ndi chabwino kwambiri.” Iye ananenanso kuti: “Ndimayamikira kwambiri kuti a Mboni amayesetsa kumasulira bwino Baibulo m’chinenero chamanja cha ku America chifukwa ndi buku lofunika kwambiri kwa anthu ndiponso m’mbiri yakale. Ndimaona kuti mabuku ofunika kwambiri ayenera kupezekanso m’chinenero chamanja kuti anthu amene ali ndi vuto losamva athe kuwawerenga.”

A Mboni za Yehova padziko lonse anamasulira mavidiyo m’zinenero zamanja pafupifupi 80 ndipo amawapereka mwaulere. Anapanganso pulogalamu ina yothandiza anthu kuti azichita dawunilodi mavidiyo a m’chinenero chamanja pa jw.org ndiponso kuwaonera mosavuta.

Lankhulani ndi:

Kuchokera Kumayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000