NOVEMBER 1, 2016
UNITED STATES
A Mboni Akukonzanso Damu ku Warwick Lomwe Lakhala kwa Zaka 60
NEW YORK—A Mboni za Yehova anamaliza kumanga likulu lawo la padziko lonse ku Warwick mu August 2016. Potsatira pulani yawo yomangira malowa, a Mboniwa amaliza ntchito yokonzanso damu lotchedwa Blue Lake. Iwo agwira ntchitoyi mothandizidwa ndi bungwe loona za madzi la SUEZ Water New York Inc.
Atangogula malowa mu 2009, a Mboniwa anapanga pulani yoti akonzenso khoma la damu la Blue Lake lomwe linali litawonongeka kwambiri. Damuli (lomwe likuoneka pachithunzi pamwambapa) lili pafupi ndi likulu latsopano la Mboni za Yehova ndipo limadziwikanso ndi dzina lakuti Sterling Forest Lake. Dipatimenti ina yosamalira zachilengedwe itapanga kafukufuku, inapeza kuti khoma la damuli linapanga ming’alu ndipo madzi amatayika. Komanso inapeza kuti zipangizo zotsekera ndi kutsegulira madzi sizimagwira ntchito zomwe zimachititsa kuti nyumba 195 zomwe zili ku Woodlands ku Tuxedo zikhale pa chiopsezo chachikulu. Nyumbazi zili pamtunda wa kilomita imodzi kuchokera ku damu la Blue Lake.
A Jeffrey Hutchinson, omwe panthawiyi anali mkulu woyang’anira malo a Sterling Forest State Park ananena kuti: “Khoma la damuli linkadonthadi moti likanangogwa pakanachitika ngozi yoopsa. Nyumba zonse zimene zili ku Woodlands zikanakokoloka ndi madziwa.”
A Robert R. Werner, omwe ndi mkulu wa bungwe lina loona za nyumba la Woodlands at Tuxedo ananena kuti: “Sindikukayikira kuti a Mboni za Yehova akanakhala kuti sanakonze damuli, palibe amene akanalikonza mwina mpaka madziwa akanasefukira. Zimenezi zikanachitika anthu ambiri akanafa komanso katundu akanawonongeka.”
A Hutchinson ananenso kuti: “M’chaka cha 2011, damu la Echo Lake lomwe lili pamtunda wa makilomita 48 kuchokera ku Blue Lake linakokolola malo otchedwa East Village ku Tuxedo ku New York.” Akatswiri amati damuli litasefukira madzi ambiri anayenda mothamanga kupita ku mtsinje wa Ramapo. Damu la Echo Lake ndi lalikulu mahekitala 5.2 ndipo ndi laling’ono poyerekeza ndi damu la Blue Lake lomwe ndi lalikulu mahekitala 46.5.
Khoma la damu la Blue Lake linamangidwa mu 1956 ndipo lili chakum’mawa kwa nyanjayi. Damuli lili ndi mbali ziwiri, mbali imodzi ndi yachilengedwe ndipo mbali ina inachita kumangidwa ndi konkire. Chitsulo chotsegulira madzi chinaikidwa pansi mudamuli. Chitsulochi chimagwiritsidwa ntchito pochepetsa madzi mudamuli ngati patachitika chinachake mwadzidzidzi.
A Richard Devine omwe ndi tcheyamani wa Komiti Yomanga Likulu la Mboni za Yehova ku Warwick, ananena kuti: “Ndife osangalala kuti ntchito yokonza damuli inayenda bwino. Tikuthokozanso bungwe loona za madzi la SUEZ chifukwa chotithandiza pa ntchitoyi. Anthu anagwira ntchito mwakhama pa damuli kuti lisagumuke. Anachotsa zitsulo zakale zotsegulira ndi kutsekera madzi n’kuika zatsopano ndipo anamanganso malo otulukira madzi. Anamanganso ndi konkire khoma lalitali loti madzi azitulukira ku mbali yopangidwa mwachilengedwe ija. Ntchitoyi yathandiza kuti damuli likhale logwirizana ndi malamulo okhudza kupewa ngozi.
A Hutchinson anafotokoza mmene amaonera a Mboni komanso ntchito imene anagwirayi. Iwo ananena kuti: “Anthu a Mboni mumagwira ntchito zambiri zothandiza anthu m’madera anu komanso mumathandiza pa ntchito zina zomwe mungathe. Ntchito zanu zomangamanga zimakhala zolimba komanso zosawononga chilengedwe.”
Lankhulani ndi:
David A. Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000
Ogwira ntchito ku Watchtower akuchotsa chitsulo chotsegulira madzi chomwe chinawonongeka mu damu la Blue Lake. Madzi akachuluka mudamuli, chitsulochi chimachotsa madzi ena kuti asasefukire.
Chitsulo chowolera zinyalala chikuikidwa pansi pa damuli. Chitsulochi chizipangitsa kuti madzi akatsegulidwa, zinyalala zisamatseke mabowo otulukira madziwo.
Ogwira ntchito ku Watchtower akukulitsa njira yodutsa madzi ya mbali yopangidwa mwachilengedwe. Madzi akatsegulidwa kuti atuluke mudamuli, azitulukira mbali yopangidwa mwachilengedwe n’kumapita m’mitsinje yomwe ili pafupi ndi damuli.
Anthu ogwira ntchito ku Watchtower anamanga ndi konkire komanso kutalikitsa ndi pafupifupi mita imodzi zipilala za mbali yotulukira madzi yopangidwa mwachilengedwe. Anakonzanso ming’alu ya khomalo.
Akuika dothi la konkire lomwe likuthandiza kuti damuli lilimbe. Panafunika dothi la konkire lokwana pafupifupi makyubiki mita 19,000.
Chithirakita chikusalaza dothi la konkire
Anthu akuonjezera dothi komanso kudzala kapinga pofuna kukongoletsa malowa.