DECEMBER 9, 2015
UNITED STATES
A Mboni za Yehova Amaliza Kumanga Mbali Yaikulu ya Likulu Lawo Latsopano Lapadziko Lonse
NEW YORK—Kuyambira mwezi wa August mpaka October, 2015, ntchito yomanga likulu latsopano la Mboni za Yehova inafika pachimake. Pamalowa pankafika anthu ogwira ntchito ongodzipereka okwana 3,800 tsiku lililonse.
Kungoyambira mu July 2013, pomwe ntchito yomangayi inayamba, a Mboni oposa 18,000 akhala akufika kumalowa kudzagwira ntchito. A Mboniwa ankachokera m’madera osiyanasiyana a dziko la United States, monga ku Alaska ndiponso Hawaii. Anthu ambiri amabwera kudzagwira ntchito pamalowa kwa mlungu umodzi, iwiri, itatu kapena 4.
A Richard Devine, omwe ndi tcheyamani wa ntchito yomanga likulu latsopano ku Warwik, ananena kuti: “Pamalo ano pamabwera anthu ambirimbiri kudzagwira ntchito. Ndiye kuti zinthu ziziyenda bwino, tinakonza zoti anthu 400 azigwira ntchito kuyambira 3 koloko madzulo mpaka 2 koloko m’mawa.” Gawo lachiwiri la ntchitoyi linagwiridwa kuyambira mwezi wa May mpaka September.
Komiti yomwe ikuyang’anira ntchitoyi inanena kuti pa nyumba zogona 4 zomwe zikumangidwa, ziwiri zikhala zitamalizidwa pofika mu January 2016 monga mmene anakonzera. Komabe a Devine ananenanso kuti: “Ntchitoyi ikufulumira kwambiri kuposa mmene tinkaganizira, moti tayamba kugwira ntchito zimene tinkayenera kudzagwira miyezi 4 ikubwerayi. Izi zatheka chifukwa anthu ambiri akudzipereka kudzagwira ntchitoyi.” Panopa ntchito yomwe yatsala ndi kumanga nyumba imodzi yogona, nyumba imodzi yomwe mudzakhale maofesi komanso nyumba yokonzeramo zinthu. Tikuyembekezera kuti ntchito imeneyi idzakhala itatha pofika pa 1 September, 2016.
Yankhulani ndi:
Kuchokera ku Mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000