14 SEPTEMBER, 2017
UNITED STATES
Amboni a ku United States Anapirira Mavuto Obwera Chifukwa cha Mphepo ya Mkuntho Yotchedwa Hurricane Harvey
Zatsopano: N’zomvetsa chisoni kuti mlongo mmodzi wachikulire mwamwalira chifukwa cha mphepo yamkuntho yotchedwa Hurricane Harvey.
NEW YORK—Lachisanu pa 25 August, 2017, mphepo yamkuntho yotchedwa Hurricane Harvey inaomba mu mzinda wa Rockport womwe uli m’mbali mwa nyanja ku Texas. Pamene limafika Lamlungu, mphepoyi inali itachepa mphamvu koma inapitirizabe kuononga kum’mwera chakum’mawa kwa Texas mpaka Lachitatu pa 30 August. Mphepoyi itangochitika, ofesi ya nthambi ku United States inalandira malipoti ofotokoza mmene mphepoyo inakhudzira abale ndi alongo athu.
Pafupifupi a Mboni okwana 84,000 amakhala m’madera amene anakhudzidwa ndi mphepo ya Harvey. Palibe wa Mboni aliyense amene wamwalira ndi mphepoyi ngakhale kuti anthu 9 anavulala ndipo ena 5 anakalandira thandizo la mankhwala ku chipatala. A Mboni okwana 5,566 analibe pokhala chifukwa nyumba zawo zinaonongeka. Mphepoyi inawononga kwambiri nyumba zokwana 475 za abale, ndipo nyumba zina 1,182 zinawonongeka pang’ono.
Ntchito yothandiza anthu amene akhudzidwa ikuyendetsedwa ndi oyang’anira madera a ku Austin, Dallas, ndi San Antonio. Abale ambiri m’mizinda imeneyi anapereka malo okhala m’nyumba zawo kwa a Mboni a ku Houston ndi Texas Gulf Coast amene nyumba zawo zinawonongeka. Enanso anapereka matani pafupifupi 300 a chakudya, madzi, ndi zinthu zina kwa anthu amene anakhudzidwa ndi mphepoyo.—Miyambo 3:27; Aheberi 13:1, 2.
Oyang’anira madera ananena kuti mipingo yonse ikupitiriza kuchita misonkhano komanso kugwira ntchito yolalikira. Abale a M’komiti ya Nthambi ya ku United States akukonza zoti akaone anthu amene anakhudzidwa n’cholinga choti akawatonthoze komanso kuwalimbikitsa.
A David A. Semonian omwe amayankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova anati: “Tili ndi chisoni chifukwa cha mavuto omwe anthu amene akhudzidwa ndi mphepo ya Hurricane Harvey akukumana nawo, ndipo tikuyamikira anthu omwe anadzipereka kuti athandize pa nthawi ya ngoziyi. Tikupempherera makamaka abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa ndi mphepo ya mkunthoyi. Tikuwalimbikitanso kuti akhale ndi chikhulupiriro kuti Yehova awathandiza.”—Salimo 55:8, 22; Yesaya 33:2; 40:11.
Lankhulani ndi:
David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000