Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku United States
Chipembedzo cha Mboni za Yehova chinayambira ku United States m’zaka za m’ma 1870, pamene Charles Taze Russell ndi anzake ena ankakumana pamodzi n’kumaphunzira Baibulo. Patadutsa zaka zingapo anayamba kufalitsa mabuku, anayambitsa bungwe lomwe linadzayamba kudziwika ndi dzina lakuti Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, ndiponso anakhazikitsa likulu lawo loyamba ku Allegheny, Pennsylvania.
A Mboni za Yehova ku United States ali ndi ufulu wochita zinthu zokhudza kulambira. Komabe, chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, anayamba kutsutsidwa kwambiri ndi akuluakulu a boma ena omwe anamva nkhani zabodza komanso ndi atsogoleri ena a zipembedzo. Pofika m’zaka za m’ma 1930 ndi m’ma 1940, a Mboni anakadandaula kumakhoti osiyanasiyana pofuna kumenyera ufulu wawo. Apolisi ankamanga a Mboni akamagwira ntchito yawo yolalikira, ana a Mboni m’dzikolo ankachotsedwa sukulu chifukwa chokana kuchitira sawatcha mbendera, ndiponso makhoti ambiri m’dzikoli ankatsekera m’ndende a Mboni omwe akana kulowa usilikali. Koma pamapeto pake Khoti Lalikulu Kwambiri ku United States linagamula nkhanizi mokomera a Mboni za Yehova.
Pofika pano, a Mboni awina milandu 50 yomwe inazengedwa ndi Khoti Lalikulu Kwambiri. Kuonjezera pamenepa, awinanso milandu yambiri m’makhoti ang’onoang’ono a m’dzikoli pa milandu yokhudza ufulu wa odwala, woyenera kusunga ana banja likatha, nkhani zokhudza malo, kusalidwa pa nkhani zokhudza ntchito komanso pa nkhani zokhudza ziphaso zoyendera. Zigamulo zokomera a Mboni zimene makhoti anapanga ku United States, zinakhudzanso malamulo oyendetsera dzikolo, ndipo a Mboni anapatsidwa ufulu wolankhula, wolemba ndi kufalitsa mabuku, wosonkhana pamodzi, komanso wopembedza. Zigamulozi zathandizanso makhoti ambiri padziko lonse kuti azigamula milandu yokhudza a Mboni mowakomera.