Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

FEBRUARY 26, 2018
UNITED STATES

Zomwe Zachitika pa Ntchito Yothandiza Anthu Omwe Anakhudzidwa ndi Mphepo Yamkuntho ya Harvey

Zomwe Zachitika pa Ntchito Yothandiza Anthu Omwe Anakhudzidwa ndi Mphepo Yamkuntho ya Harvey

NEW YORK—Zinthu zikuyambiranso kuyenda bwino kwa anthu omwe amakhala ku Texas, U.S.A., pambuyo pa mphepo yamkuntho ya Harvey yomwe inawononga zinthu kufupi ndi Corpus Christi pa 25 August, 2017. Ntchito yothandiza abale ndi alongo ambiri omwe anakhudzidwa ndi mphepoyi ikuyendetsedwa ndi makomiti awiri othandiza pakachitika ngozi zamwadzidzidzi.

M’bale akufunafuna a Mboni za Yehova kumalo othandizira anthu okhudzidwa ndi ngozi ku Houston, Texas.

Anthu ongodzipereka oposa 7,000 anathandiza nawo pa ntchito yoyeretsa nyumba pafupifupi 2,300 za ofalitsa. Ndipo mlungu uliwonse pali anthu pafupifupi 1,000 omwe amadzipereka kukagwira ntchito yomanga nyumba zoonongeka. Pofika pano, amaliza kukonza Nyumba za Ufumu zokwana 48, komanso miyezi ikubwerayi akuyembekezera kukonza nyumba za anthu zopitirira 545. Zikuoneka kuti ntchitoyi itenga ndalama zokwana madola 8.5 miliyoni a ku America ndipo itha pofika pa 30 June 2018.

Kungoyambira kumapeto kwa mwezi wa August 2017, abale oposa 22 oimira nthambi komanso abale 7 a Mukomiti ya Nthambi akhala akupita kumadera omwe kunachitika mphepo yamkunthoyi kukalimbikitsa mwauzimu ofalitsa onse okhudzidwa ndi ngoziyi. Ndi pemphero lathu kuti onse amene akugwira nawo ntchito yothandiza abale athuwa ‘adzalimbitsidwa manja’ kuti agwire bwino ntchitoyi.—Nehemiya 6:9.

Ogwira ntchito yothandiza pakachitika ngozi zadzidzidzi ku Aransas Pass, Texas.

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000