MAY 30, 2019
UZBEKISTAN
Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu Unachitika Mosabisa ku Uzbekistan
Pa 19 April, 2019, abale athu m’madera onse a m’dziko la Uzbekistan anachita mwambo wokumbukira imfa ya Khristu. Aka kanali koyamba kuchita mwambowu mosabisa m’zaka zaposachedwapa.
A Mboni za Yehova ku Uzbekistan anawalola kulembetsa chipembedzo chawo mumzinda wa Chirchik wokha, womwe uli pafupi ndi mzinda wa Tashkent lomwe ndi likulu la dzikolo. M’mbuyomu, abale athu omwe sakhala mumzinda wa Chirchik ankachita mwambowu mobisa popewa kusokonezedwa ndi apolisi. Chaka chino, abalewa anadziwitsa apolisi za mwambo wokumbukira imfa ya Yesu n’kuwaitaniranso kumwambowu. Apolisiwo anavomera ndipo anaonetsetsa kuti anthu omwe anapezeka pamwambowu ndi otetezeka. M’madera ena, apolisi anakhala nawo pamwambowu.
M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani ya Chikumbutso m’Nyumba ya Ufumu ina ku Chirchik monga mmene chithunzi choyambirira chikusonyezera. Mwambowu unamasuliridwa m’Chirasha. Anthu onse omwe anapezekapo anali 781. Pambuyo pake, mipingo inanso iwiri inachita mwambowu motsatizana m’Nyumba ya Ufumu yomweyi.
Pa ulendowu, M’bale Sanderson anali limodzi ndi m’bale Paul Gillies wochokera kulikulu la padziko lonse komanso abale awiri ochokera ku Central Asia. Abalewa anakumana ndi akuluakulu a ku Unduna Wazachilungamo ndiponso a bungwe loona za ufulu wachibadwidwe (National Centre for Human Rights). Pa nthawi yomwe ankakambirana ndi akuluakuluwa, abale athuwa anapatsidwa mwayi wofotokoza mfundo zolondola zokhudza gulu lathu komanso zimene timakhulupirira. Tikukhulupirira kuti akuluakuluwa akadziwa zambiri za gulu lathu, adzathandiza kuti tivomerezedwe kulembetsa chipembedzo chathu m’madera enanso osati ku Chirchik kokha. Zimenezi zidzathandiza kuti abale athu akhale ndi malo olambirira oyenerera.
Kuchita mwambo wa Chikumbutso mosabisa komanso kukambirana bwino ndi akuluakulu a boma zomwe zachitika ku Uzbekistan posachedwapa, ndi zinthu zosangalatsa kwambiri. M’miyezi 6 yapitayi, a Mboni za Yehova sanathyoleredwe nyumba zawo, kulipitsidwa chindapusa kapena kumangidwa. Komanso pafupifupi chaka chimodzi chapitacho, pa 14 May, 2018, kazembe wa dziko la Uzbekistan ku United States, a Javlon Vakhabov ananena poyera kuti nyumba ya malamulo idzayesetsa kusintha malamulo n’cholinga choti a Mboni za Yehova asamavutike kulembetsa chipembedzo chawo kuti chikhale chovomerezeka ndi boma.
Tikuyembekezera Yehova kuti adalitse khama la abale athu ku Uzbekistan pamene akupitiriza kukhala ndi ‘moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti akhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira komanso akhale oganiza bwino.’—1 Timoteyo 2:2.