Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Uzbekistan
A Mboni za Yehova anakhala akupezeka ku Uzbekistan kwa zaka zambiri dzikoli lisanalandire ufulu wodzilamulira mu 1991. Mu 1992, dziko la Uzbekistan linakhazikitsa malamulo omwe ankapereka maufulu osiyanasiyana kwa anthu. Komabe, pa nkhani ya ufulu wachipembedzo, boma nthawi zambiri limanyalanyaza mfundo zikuluzikulu za m’malamulowo.
Akuluakulu a boma la Uzbekistan akupitiriza kukana kulemba mipingo yonse ya Mboni za Yehova kuti ikhale yovomerezeka kupatulapo umodzi wa ku Chirchik. a Chifukwa cha zimenezi, msonkhano uliwonse wachipembedzo womwe a Mboni angachitire pamalo ena osati m’Nyumba ya Ufumu ku Chirchik, umaonedwa kuti ndi wosemphana ndi malamulo. Nthawi zambiri apolisi amasokoneza misonkhano yachipembedzo ya a Mboni ikachitikira pamalo ena, ngakhale m’nyumba za anthu. Akuluakulu a boma amamanga anthu omwe ali pamsonkhanopo ndiponso kulanda zinthu zawo komanso mabuku a chipembedzo. Akuluakulu ena a boma amasunga a Mboni ena kwa masiku ambiri, amawazunza komanso kuwayankhula mwachipongwe. A Mboni ena alipitsidwa ndalama zambiri za chindapusa, kuwapeza olakwa, komanso kuwalamula kuti akhale m’ndende kwa zaka chifukwa chochita zinthu zokhudza chipembedzo chawo. Chifukwa choti boma linakana kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova chilembetsedwe kukhala chovomerezeka, zimachititsa kuti a Mboni aziimbidwa mlandu akachita chilichonse chokhudza chipembedzo chawo.
A Mboni za Yehova akupitiriza kukambirana ndi oimira boma n’cholinga choti awalole kulembetsa mipingo yawo ya m’dziko lonse la Uzbekistan, makamaka ku Tashkent. Ngati zimenezi zingatheke, ndiye kuti a Mboni akhoza kukhala otetezeka ku tsankho lomwe amawachitira komanso zilimbikitsa anthu kuti azilemekeza ufulu wopembedza womwe a Mboni ali nawo.
a Mpingowu unalembetsedwa koyamba mu 1994 kenako unalembetsedwanso mu 1999.