Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 6, 2019
VENEZUELA

Mmene Zinthu Zilili Panopa ku Venezuela: Ntchito ya a Mboni za Yehova Ikupitabe Patsogolo Ngakhale Kuti Mavuto Sakutha

Mmene Zinthu Zilili Panopa ku Venezuela: Ntchito ya a Mboni za Yehova Ikupitabe Patsogolo Ngakhale Kuti Mavuto Sakutha

Mavuto azachuma komanso kusokonekera kwa zinthu zikupitirirabe ku Venezuela. Anthu akuvutika kwambiri kupeza chakudya, madzi, mafuta a galimoto komanso mankhwala chifukwa cha kusowa kwa zinthuzi ndiponso kukwera kwa mitengo. Kuzimazima kwa magetsi kukuchititsa kuti chakudya chizisowa chifukwa sichingasungidwe m’mafiriji magetsi akazima. Vuto linanso lomwe likudetsa nkhawa ndi zaupandu zomwe zikuchitika kawirikawiri.

Ngakhale kuti zinthu zafika poipa chonchi, ofalitsa oposa 136,500 ku Venezuela akupitirizabe kugwira ntchito yolalikira mwakhama. Mwachitsanzo, mu January 2019 chiwerengero cha ofalitsa m’dzikoli chinali chitachepa ndi ofalitsa 7,000 poyerekezera ndi chaka chatha. Komabe, iwo analalikira maola owonjezera okwana 90,000 poyerekeza ndi maola a chaka chatha. Mu April 2019, iwo anachititsa maphunziro a Baibulo oposa 195,600. Chiwerengero cha apainiya okhazikika chinakwera ndipo chinaposa 30,000. Chifukwa cha ntchito yapadera yoitanira anthu ku Chikumbutso cha imfa ya Khristu yomwe inachitikanso padziko lonse, chiwerengero cha apainiya othandiza chinawonjezeka kufika pa 20,400. Zotsatirapo zake zinali zoti anthu pafupifupi 471,000 anapezeka pa Chikumbutso ndipo chiwerengerochi ndi kuwirikiza katatu chiwerengero cha ofalitsa. Kuwonjezera pamenepa, anthu ambiri akumapezeka nawo pamisonkhano yampingo chifukwa choti abale ndi alongo akupitiriza kugwira ntchito yolalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu omwe akufunafuna njira yodalirika yothetsera mavuto awo.

Ofesi ya nthambi ya Venezuela ikupitiriza kuyendetsa ntchito yopereka chakudya pothandiza abale athuwa. Mwezi uliwonse, ofesi ya nthambi ya Venezuela imagawa chakudya cholemera matani mahandiredi ambirimbiri kwa ofalitsa 75,000 omwe ali m’mipingo 1,595. Ofesiyi imachita zimenezi mothandizidwa ndi maofesi a nthambi oyandikana nayo komanso pogwiritsa ntchito ndalama zothandizira ntchito ya padziko lonse zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo.

Abale athu ku Venezuela akukumana ndi mavuto ambiri koma n’zolimbikitsa kuti akupitiriza ‘kukondwerabe mwa Yehova ndipo akusangalala mwa Mulungu wachipulumutso chawo.’—Habakuku 3:17, 18.