Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Abale ndi alongo athu ku Venezuela akupitirizabe kukhala olimba chifukwa choti amasonkhana komanso amalalikira mwakhama.

NOVEMBER 5, 2018
VENEZUELA

Mmene Zinthu Zilili Panopa ku Venezuela: A Mboni Ndi Okhulupirikabe Ngakhale Akukumana ndi Mavuto a Zachuma

Mmene Zinthu Zilili Panopa ku Venezuela: A Mboni Ndi Okhulupirikabe Ngakhale Akukumana ndi Mavuto a Zachuma

Abale ndi alongo athu ku Venezuela akupitirizabe kuvutika chifukwa cha mavuto a zachuma omwe dzikolo likukumana nawo. Mlungu uliwonse ofesi ya nthambi ku Venezuela imalandira malipoti okhudza abale amene achitiridwa nkhanza zosiyanasiyana. Komanso mbava zakhala zikuthyola ndi kuba zinthu m’Nyumba za Ufumu zambiri m’dzikolo. Mavuto enanso amene abale athu akulimbana nawo ndi monga kukwera kwambiri mitengo kwa zinthu, kusowa kwa chakudya, mankhwala, ndi zinthu zina zofunika. Kuyambira mu 2013, ofalitsa oposa 20,000 akhala akuthawira ku mayiko ena monga Argentina, Brazil, Chile, Colombia, Ecuador, Italy, Peru, Portugal, Spain, ndi United States. a Ngakhale kuti ku Venezuela kukuchitika mavuto onsewa, a Mboni za Yehova pafupifupi 140,000 omwe adakali m’dzikoli, akutumikirabe Yehova mwakhama.

Ofesi ya nthambi ku Venezuela ikupitirizabe kuthandiza abale ndi alongo omwe akukumana ndi mavuto m’dzikolo. Panopa pali makomiti othandiza anthu okwana 60 omwe cholinga chawo chachikulu ndi kupereka chakudya kwa abale ndi alongo. Pofika pano, ofesi ya nthambi ku Venezuela mothandizidwa ndi ofesi ya nthambi ya ku Brazil, yagawa chakudya chochuluka kwa ofalitsa oposa 64,000 a m’mipingo yokwana 1,497. Chakudyachi n’chomwe a Mboni ena anapereka pofuna kuthandiza abale ndi alongo awo.

Ofesi ya nthambi ya Venezuela ikupitirizanso kuthandiza abale ndi alongo kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova komanso kuti azimutumikira. Mwachitsanzo, m’dzikoli munachitika misonkhano ya chigawo ya mutu wakuti “Limbani Mtima” yokwana 122, ndipo womaliza unachitika kuyambira pa 31 August mpaka pa 2 September, 2018. Misonkhanoyi inalimbikitsa kwambiri abale ndi alongo athu ngakhale kuti ambiri anavutika kwambiri kuti apeze ndalama zowathandiza kuti akapezeke kumisonkhanoyi.

Panopa a Mboni ku Venezuela akuyesetsa kuthandiza anthu ambiri amene akukumana ndi mavutowa powalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo. Ofalitsa akuchititsa maphunziro a Baibulo pafupifupi 200,000 mwezi ulionse. Chiwerengero cha anthu atsopano amene akusonkhana nachonso chikukwera ndipo anthu 7,259 anabatizidwa.

Zinthu zabwinozi zomwe zikuchitika m’gulu la Yehova, zikusonyeza kuti Mulungu akugwiritsa ntchito mzimu wake pothandiza abale ndi alongo athu ku Venezuela kuti akhale olimba. Ndi pemphero lathu kuti abale athuwa apitirize kudalira Yehova mpaka pa nthawi imene Ufumu wake udzachotse mavuto onse omwe alipowa.—Miyambo 3:5, 6.

Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene zinthu ziliri ku Venezuela, onerani vidiyo yakuti Abale Athu ku Venezuela Akusonyeza Chikondi Komanso Chikhulupiriro pa Nthawi Yovuta Kwambiri.

a M’dziko mukakhala mavuto a zachuma, zipolowe kapenanso mavuto a zandale, wofalitsa aliyense ayenera kusankha yekha ngati akufuna kuthawa kapena kukhalabe m’dzikolo. Gulu la Yehova sililimbikitsa kapena kuletsa munthu kuthawa kapena kukhalabe m’dzikolo.—Agalatiya 6:5.