25 OCTOBER 2021
ZAMBIA
Baibulo Latulutsidwa M’chinenero cha Chilunda
Pa 16 October 2021, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika linatulutsidwa m’chinenero cha Chilunda pa pulogalamu yapadera imene inaonetsedwa pa intaneti m’mayiko atatu a ku Africa. Baibuloli linatulutsidwa la pazipangizo zamakono zokha ndipo losindikizidwa liyamba kupezeka cha mu February 2022.
M’bale Emmanuel Chiposa, wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Zambia, anakamba nkhani yochita kujambulidwa pamene ankatulutsa Baibuloli. Anthu a ku Angola, Democratic Republic of the Congo komanso Zambia anaonera nkhaniyi kudzera pa intaneti.
Anthu olankhula Chilunda amakonda kulima chimanga, chinangwa komanso mbatata. Ku Zambia, amakhala pafupi ndi mtsinje wotchuka wa Zambezi, omwe ndi mtsinje waukulu wa nambala 4 ku Africa pambuyo pa Nile, Congo, ndi Niger. A Mboni za Yehova anayamba kulalikira kwa anthu a Chilunda cha m’ma 1930, ndipo anayamba kumasulira mabuku a m’chilankhulochi mu 2003.
Mu September 2019, timu ya omasulira ya Chilunda inasamukira ku maofesi atsopano a omasulira mabuku. Kusamukaku kunawathandiza abalewa m’njira zambiri, imodzi inali yakuti anasamukira kumalo amene intaneti sivutavuta.
Kwa zaka zambiri abalewa ankadalira Mabaibulo odula, omwenso anali ovuta kumvetsa komanso osowa. Baibulo la Dziko Latsopano la Chilunda linamasuliridwa molondola ndipo ndi losavuta kumva. Mwachitsanzo, mawu a pa Genesis 3:15, akuti “mbewu,” m’Mabaibulo ena a Chilunda amatanthauza mbewu zambirimbiri. Zimenezi zinkachititsa kuti ofalitsa azivutika kufotokoza kuti ulosiwu ukunena za Yesu. Koma Baibulo la Dziko Latsopano la Chilunda linamasulira molondola mawu amenewa.
Omwe anagwira ntchito yomasulira Baibuloli anasangalala kwambiri litatulutsidwa. Mmodzi mwa iwo ananena kuti: “Tikukhulupirira kuti anthu akawerenga Baibuloli aona kuti Mlengi wawo Yehova amawakonda kwambiri.”
Kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Chilunda ndi umboni wakuti Yehova amakonda anthu a mitundu yonse. Baibuloli lithandiza anthu a Yehova kupitiriza kulengeza uthenga wa Ufumu mpaka “kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.”—Aroma 10:18.