APRIL 22, 2019
ZIMBABWE
A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso la Chishona
Pa 17 March, 2019, M’bale Kenneth Cook wa m’Bungwe Lolamulira, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso la chinenero cha Chishona pamsonkhano wapadera womwe unachitikira pa Malo a Msonkhano a Harare ku Zimbabwe. Ntchito yomasulira Baibuloli inatenga zaka zitatu.
Abale ndi alongo pafupifupi 2,500 anapezeka ku Malo a Msonkhanowo pamene Baibuloli linkatulutsidwa. Abale ndi alongo enanso 43,000 anaonera msonkhanowu m’Nyumba za Ufumu 295 ndi m’Malo a Misonkhano 4. M’bale wina anati: “Ndikufunitsitsa kugwiritsa ntchito Baibulo lokonzedwanso limeneli muutumiki. Alilemba m’njira yosavuta kumva komanso yosangalatsa, zomwe n’zochititsa munthu kuti azingoliwerengabe. Tikuthokoza Yehova chifukwa cha mphatsoyi.”
Baibuloli lithandiza ofalitsa 38,000 omwe amatumikira m’dera la Chishona. Komanso, liwathandiza polalikira kwa anthu oposa 9 miliyoni omwe amalankhula chinenerochi, omwe ndi pafupifupi 80 peresenti ya chiwerengero cha anthu ku Zimbabwe.
Pa nthawi iliyonse imene Baibulo latulutsidwa, umakhala umboni woti Yehova akudalitsa khama lomwe limakhalapo pa ntchito yomasulira yomwe ikuchitika padziko lonse. Tikusangalala kuti Mawu ake akupezeka m’zinenero zobadwira za anthu ambiri.—Machitidwe 2:8.