Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

N’chifukwa Chiyani Ndilibe Anzanga Enieni?

N’chifukwa Chiyani Ndilibe Anzanga Enieni?

Yerekezani kuti muli pa Intaneti ndipo mukuona zithunzi za pate imene yachitika chaposachedwa. Pazithunzipo mukuonapo anzanu ndipo zikuchita kusonyezeratu kuti anasangalala kwambiri. Koma mukayang’anitsitsa pazithunzipo, mukuona kuti inuyo palibepo.

Ndiye mukudabwa kuti: ‘N’chifukwa chiyani anzangawa sanandiitane?’

Kenako zayamba kukupwetekani poona kuti anzanu sanakuitaneni. Mukuona kuti anthu amene mumawawerengera kuti ndi anzanu akugwiritsani mwala. Ndiyeno mukuona kuti mulibiretu mnzanu woti mungamacheze naye ndipo mukudzifunsa kuti ‘N’chifukwa chiyani ndilibe anzanga enieni?’

 Mafunso okhudza kusowa anthu ocheza nawo

 Zoona Kapena Zonama

  1.   Ngati muli ndi anzanu ambiri, simungasowe munthu wocheza naye.

  2.   Ngati mutayamba kucheza ndi anthu pa Intaneti, simungasowe munthu wocheza naye.

  3.   Ngati mungamatumize mameseji ambirimbiri a pafoni kwa anthu osiyanasiyana, simungasowe munthu wocheza naye.

  4.   Ngati mumathandiza anthu m’njira zosiyanasiyana, simungasowe munthu wocheza naye.

 Yankho la zonsezi ndi lakuti zonama.

 Chifukwa chiyani zili choncho?

 Zoona zake pa nkhani ya kupeza kapena kusowa anthu ocheza nawo

  •   Kukhala ndi anthu ambiri ocheza nawo sizitanthauza kuti basi munthu sangasowe wocheza naye.

     “Anzanga ndimawakonda kwambiri koma nthawi zina ndimaona kuti iwowo sandikonda. Zimakhala zowawa kwambiri ukakhala kuti uli ndi anzako ambiri amene ukuona kuti ungamacheze nawo koma n’kupezeka kuti iwowo sasonyeza kuti amakukonda kapena kukusowa.”​—Anne.

  •   Kuyamba kucheza ndi anthu pa Intaneti sizitanthauza kuti basi munthu sangasowe wocheza naye.

     “Anthu ena amapeza anzawo ambirimbiri ngati mmene anthu ena amakhalira ndi zidole zambirimbiri. Koma munthu ngakhale atakhala ndi zidole zambiri bwanji, zidolezo zisingamusonyeze kuti zimamukonda. Ndiye ngati munthu ulibe anzako odalirika, kucheza ndi anthu pa Intaneti sikungakuthandize kuona kuti umakondedwa. Zili ngati kukhala ndi zidole zambirimbiri zomwe sizingakusonyeze kuti zimakukonda.”​—Elaine.

  •   Kutumiza mameseji ambirimbiri sikutanthauza kuti simungasowe wocheza naye.

     “Nthawi zina ukakhala kuti ukusowa munthu wocheza naye, umangoyang’ana pafoni nthawi ndi nthawi kuti uone ngati pali mnzako amene wakutumizira meseji. Ndiye zikakhala kuti palibe amene wakutumizira meseji, umaona kuti palibiretu mnzako amene amakusowa.”​—Serena.

  •   Kuthandiza anthu m’njira zosiyanasiyana sizitanthauza kuti basi munthu sungasowe wocheza naye.

     “Ndimayesetsa kupereka mphatso kwa anzanga, koma ndikuona kuti iwowo sandipatsa kanthu. Sikuti ndikudandaula ayi, koma zimadabwitsa kuti iwowo sandichitira zinthu ngati zimene ineyo ndimawachira.”​—Richard.

 Mfundo yofunika kwambiri: Ukamasowa anthu ocheza nawo, nthawi zambiri vuto limagona pa mmene munthuwe umaonera zinthu. Pa mfundoyi, mtsikana wina dzina lake Jeanette ananena kuti: “Kwenikweni vuto limagona pa zimene iweyo umaganiza, osati pa zimene zikuchitika.”

 Kodi mungatani ngati mumaona kuti mulibe anzanu ndipo mumasowa wocheza naye?

 Zimene mungachite kuti muthane ndi vutoli

Musamadzikayikire.

 “Munthu ukakhala kuti umadzikayikira, ukhoza kumasowa anthu ocheza nawo. Zimavuta kuyamba kucheza ndi anthu ngati iweyo umadziona kuti ndiwe wosafunika komanso kuti palibe amene angafune kucheza nawo.”​—Jeanette.

 Baibulo limati: “Uzikonda mnzako ngati mmene umadzikondera wekha.” (Agalatiya 5:14) Kuti tizisangalala kucheza ndi anzathu, tikufunika kumadziona kuti ndife ofunika. Koma izi sizikutanthauza kuti tizinyada.​—Agalatiya 6:3, 4.

Musamangodandaula zilizonse

 “Kusowa munthu wocheza naye kuli ngati kutitimira m’matope. Ukamalowa kwambiri m’matope, zimakhalanso zovuta kutulukamo. Choncho mukamangokhalira kudandaula kuti palibe munthu amene amafuna kucheza nanu, mukhoza kukhala wosasangalala ndipo sipangapezeke munthu amene angafune kucheza nanu.”​—Erin.

 Baibulo limati: “Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.” (1 Akorinto 13:4, 5) Apa mfundo ndi yakuti tikamaganizira mopitirira malire mavuto athu, sitingakwanitse kuchitira chifundo anthu ena ndipo zimenezi zimachititsa kuti anthu asamakonde kucheza nafe. (2 Akorinto 12:15) Dziwani izi: Ngati mumaganiza zoti, kuti zinthu zikuyendereni bwino zikudalira zimene anthu ena amachita, ndiye kuti palibe chimene chingakuyendereni. Mukamangodandaula kuti “Palibe amene amandiimbira foni,” kapena “Palibe amandiitana kocheza,” ndiye kuti mumadalira anthu ena kuti mukhale wosangalala. Kuchita zimenezi n’chimodzimodzi n’kuwapatsa mphamvu anzanuwo zoti azikulamulirani.

Musamangosankha anzanu mwachisawawa.

 “Anthu amene amasowa anzawo amafuna munthu amene angawasonyeze kuti amawaganizira. Ndiye aliyense akangowasonyeza kuti ndi ofunika komanso akuwaganizira, basi amangoti mnzanga ndi ameneyu. Koma anthu ena akhoza kukusonyezani kuti ndinu wofunika kenako n’kuyamba kukudyerani masuku pamutu. Mapeto ake mukhoza kudziona kuti ndinu wosafunika kuposa poyamba.”​—Brianne.

 Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” (Miyambo 13:20) Munthu amene watsala pang’ono kufa ndi njala akhoza kudya chakudya chilichonse. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene akusowa wocheza naye. Iye akhoza kumangocheza ndi munthu aliyense. Zotsatira zake n’zakuti amayamba kucheza ndi anthu olakwika, amene angamulowetse m’mavuto.

 Mawu omaliza: Munthu aliyense nthawi zina amasowa wocheza naye, ndipo munthu angavutike kwambiri mumtima ngati akusowa wocheza naye. Komabe tisaiwale kuti kusowa wocheza naye kumadalira pa mmene munthuyo akuonera zinthu komanso mmene akuganizira. Choncho n’zotheka kusankha zimene tikufuna kuganiza.

 Mukuyeneranso kupewa kuyembekezera kuti anthu ena azikuchitirani zinthu zimene sizingatheke. Jeanette amene tamutchula poyamba paja ananena kuti: “Sikuti munthu aliyense angakhale mnzako wapamtima mpaka kalekale. Komabe pamapezeka anthu ena amene amakukonda. Kukumbukira zimenezi kumathandiza kuti usamadandaule n’zoti ukusowa anthu ocheza nawo.”

 Kodi mukufuna kudziwa zambiri pa nkhaniyi? Werengani nkhani yakuti “ Musaope Kupeza Anzanu Atsopano.” Mukhozanso kukopera nkhani yakuti “Kulimbana ndi Vuto Losowa Wocheza Naye.”