ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
N’chiyani Chingandithandize Ndikakhala Ndi Nkhawa?
N’chiyani chimakuchititsani kuti muzida nkhawa?
Kodi zinthu zimene zafotokozedwa m’munsimu zimakuchitikirani nthawi zina?
“Nthawi zambiri ndimaganiza kuti: ‘Kodi ndingatani ngati . . . ?’ Mwachitsanzo, ‘Kodi ndingatani ngati galimoto ndakwerayi itachita ngozi?’ ‘Kodi ndingatani ngati ndege takwerayi itagwa?’ Ndimada nkhawa ndi zinthu zoti munthu wina sangade nazo nkhawa kwambiri.”—Charles.
“Nthawi zonse ndimada nkhawa ngati ndine khoswe amene watsekeredwa m’katoni ndipo akusowa kopita. Ndimagwira ntchito mwakhama koma sizimayenda.”—Anna.
“Anthu akandiuza kuti ndili ndi mwayi chifukwa ndidakali pa sukulu, mumtimamu ndimangoti, ‘akanadziwa mmene sukulu imabowera!’”—Daniel.
“Nthawi zonse ndimaona kuti ndili ndi zochita zambiri moti ndimada nkhawa ndi zinthu zimene ndiyenera kuchita kapena zimene zingandichitikire.”—Laura.
Dziwani izi: Baibulo limanena kuti tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Zimenezi zingachititse kuti achinyamata ndi akuluakulu omwe azida nkhawa.
Kodi kuda nkhawa ndi kolakwika nthawi zonse?
Ayi, chifukwa Baibulo limanena kuti sikulakwa ngati munthu akuda nkhawa chifukwa cha zimene angachite kuti asangalatse anthu amene amawakonda.—1 Akorinto 7:32-34; 2 Akorinto 11:28.
Komanso kuda nkhawa kungatithandize kuti tichite bwino zinthu zina. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mulemba mayeso mlungu wamawa. Kuda nkhawa ndi mayesowo kungakuchititseni kuti mlungu uno muwerenge kwambiri, zomwe zingakuthandizeni kuti mudzakhoze bwino mayesowo.
Nthawi zina kuda nkhawa kungakuthandizeninso kupewa zinthu zoopsa. Mtsikana wina dzina lake Serena ananena kuti: “Ukadziwa kuti ukuchita zinthu zoipa umakhala ndi nkhawa. Zimenezi zingathandize kuti usiye zoipazo n’cholinga choti usakhalenso ndi nkhawa chifukwa chodziimba mlandu.”—Yerekezerani ndi Yakobo 5:14.
Dziwani izi: Kuda nkhawa kungakhale kwaphindu kwa inu ngati kukukuthandizani kuchita zinthu zabwino.
Kodi mungatani ngati kuda nkhawa kukuchititsa kuti muzidziona kuti ndinu wosafunika?
Chitsanzo: Mnyamata wina wazaka 19, dzina lake Richard ananena kuti: “Ndikakhala kuti ndikuganizira zotsatira za zinthu zodetsa nkhawa m’pamene ndimada nkhawa kwambiri. Ndimaganizira zinthu zosiyanasiyana zimene zingachitike ndipo mapeto ake zimandidetsa nkhawa kwambiri.”
Baibulo limanena kuti “mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” (Miyambo 14:30) Kuda nkhawa kungabweretse mavuto osiyanasiyana monga kupweteka kwa mutu, chizungulire, kupweteka kwa m’mimba komanso matenda a mtima.
Kodi mungatani ngati kuda nkhawa kukukubweretserani mavuto m’malo mokuthandizani?
Zimene Mungachite
Muyenera kudziwa ngati zimene mukudandaulazo zilidi zodetsa nkhawa. “Kudera nkhawa zimene mungachite kuti mukwanitse udindo wanu ndi kosiyana ndi kumangoda nkhawa pa zifukwa zosayenera. Mfundo imeneyi imandikumbutsa mawu akuti, nkhawa ili ngati munthu amene akugwira ntchito yokatunga madzi n’kumathira m’diramu lobooka. Kuda nkhawa kwambiri kungangotiwonongera nthawi ndipo n’kosathandiza.”—Katherine.
Baibulo limati: “Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?”—Mateyu 6:27.
Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Ngati kuda nkhawa sikukuthandizani kupeza njira yothetsera vuto lanu, kungangowonjezera vutolo kapenanso kuda nkhawako kungakubweretsereni mavuto.
Musamade nkhawa ndi zinthu zimene sizinachitike. “Ndibwino kumadzifunsa kuti kodi zimene ndikuda nazo nkhawa lerozi, ndidzada nazobe nkhawa pakapita tsiku, mwezi, chaka kapena zaka 5?”—Anthony.
Baibulo limati: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”—Mateyu 6:34.
Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Si nzeru kumadera nkhawa kwambiri zinthu za mtsogolo zomwe zina sizingachitike n’komwe.
Kuvomereza kuti sitingakwanitse kuchita zinthu zina n’kothandiza. “Ndibwino kuchita zimene tingathe kuti tisakumane ndi vuto koma tiyenera kuvomereza mfundo yakuti pali zinthu zina zimene sitingakwanitse kuchita.”—Robert.
Baibulo limati: “Anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano,. . . ngakhale odziwa zinthu sakondedwa, chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.”—Mlaliki 9:11.
Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Nthawi zina sizingatheke kusintha mmene zinthu zilili pa moyo wanu koma n’zotheka kusintha mmene mumaonera zinthuzo.
Muziganizira zinthu zofunika kwambiri. “Ndimaona kuti kumvetsa bwino zinthu zonse zomwe zikukuchitikira n’kothandiza m’malo mongoganizira zinthu zing’onozing’ono zokha. Ndimaganizira zinthu zimene zili zofunika kwambiri n’kuthana nazo.”—Alexis.
Baibulo limati: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.
Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Anthu amene amaganizira zinthu zofunika kwambiri sakhala ndi nkhawa zochuluka.
Muziuzako ena. “Ndili sitandade 6, ndikaweruka ndinkakhala ndi nkhawa ndikaganizira kuti mawa ndipitanso kusukulu. Ndinkafotokozera mayi ndi bambo anga nkhawa zanga ndipo ankandimvetsera mwachidwi. Zimenezi zinkandithandiza kuti ndisamade nkhawa kwambiri. Ndinkawafotokozera chilichonse momasuka ndipo tsiku lotsatira sindinkakhala ndi nkhawa.”—Marilyn.
Baibulo limati: “Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.”—Miyambo 12:25.
Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Makolo anu kapena anzanu akhoza kukupatsani malangizo othandiza kuti muchepetse nkhawa zimene muli nazo.
Muzipemphera. “Ndimapemphera motulutsa mawu ndipo zimenezi zimandithandiza kwambiri. Zimapangitsa kuti ndizilankhula zimene zikundidetsa nkhawa m’malo mozisunga mumtima. Zimandithandizanso kuzindikira kuti Yehova ndi wamkulu kuposa zinthu zimene zikundidetsa nkhawazo.”—Laura.
Baibulo limati: ‘Mutulireni nkhawa zanu zonse [Mulungu], pakuti amakuderani nkhawa.’—1 Petulo 5:7.
Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Kupemphera si njira yothetsera mavuto patokha koma ndi njira yolankhulirana ndi Yehova Mulungu. Iye analonjeza kuti: “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.”—Yesaya 41:10.