ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kukhala Pachibwenzi—Mbali Yachitatu: Kodi Ndithetse Chibwenzichi?
Mwakhala muli pachibwenzi kwa nthawi ndithu koma mwayamba kukayikira zinthu zina. Kodi mupitirize chibwenzicho kapena mungochithetsa? Nkhaniyi yalembedwa kuti ikuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita.
Zimene zili munkhaniyi
Kodi mungatani ngati pali zokayikitsa?
Pambuyo pokhala pachibwenzi kwa nthawi ndithu, mnyamata ndi mtsikana angayambe kuona kuti si oyenererananso ngati mmene ankaganizira pamene ankayamba chibwenzi chawo. Mwachitsanzo:
Wina amakonda kukasangalala kunyanja; wina amakonda kukwera mapiri.
Wina amakonda kucheza; wina sakonda zolankhulalankhula.
Wina amakonda kuchita zinthu mwachinyengo; wina amachita zinthu moona mtima nthawi zonse.
Mungaone kuti zochitikazi zili m’magulu osiyana. Chitsanzo choyambacho chikusonyeza kuti anthu awiriwo amakonda zinthu zosiyana; chachiwiri chikusonyeza kuti anthu awiriwo amasiyana zochita; chachitatu chikusonyeza kuti anthu awiriwo ali ndi maganizo osiyana pa nkhani ya mmene amaonera makhalidwe abwino.
Zoti muganizire: Pa magulu atatuwa, kodi mukuona kuti ndi munthu uti amene mungadzavutikane naye mutati mwakwatirana naye? Nanga ndi mbali iti imene mukuona kuti nonse mungakwanitse kusintha?
Mwamuna ndi mkazi omwe ndi okwatirana angasiyane zokonda kapena zochita, komabe angathe kukhala ndi banja losangalala. Ndipotu kukhala oyenererana sikutanthauza kuti muzichita zinthu mofanana nthawi zonse. Nthawi zina, anthu okwatirana amayamba kukonda zimene mnzawo amakonda kapenanso amayamba kuona ubwino wa zochita za mnzawo. a
Komabe, ndi bwino kuti munthu amene mukufuna kukwatirana naye akhale ndi maganizo ofanana ndi anu pa nkhani ya mmene amaonera makhalidwe abwino monga zimene mumakhulupirira pa nkhani ya chipembedzo, makhalidwe komanso mmene amaonera zoyenera ndi zosayenera. Ngati mukusiyana pa mbali imeneyi, dziwani kuti chimenechi ndi chizindikiro chakuti mukufunika kuthetsa chibwenzicho.
Mwachitsanzo, tiyeni tione kusiyana komwe kulipo pa nkhani ya chipembedzo. Buku lina la Chingelezi la mutu wakuti Fighting for Your Marriage, limanena kuti: “Kafukufuku akusonyeza kuti mabanja omwe ndi osiyana zipembedzo nthawi zambiri sachedwa kutha.”
Mfundo ya m’Baibulo: “Musayerekeze kuchitira zinthu limodzi ndi osakhulupirira ngati kuti ndinu ofanana, chifukwa zimenezi n’zosatheka.”—2 Akorinto 6:14, Good News Translation.
Kusankha zochita
Baibulo limanena kuti anthu amene asankha kukwatira “adzakhala ndi masautso komanso chisoni.” (1 Akorinto 7:28, The New English Bible) Choncho, musamadabwe mukamakumana ndi mavuto ngakhale pamene muli pachibwenzi.
Si nthawi zonse pamene kusiyana maganizo pa zinthu zing’onozing’ono kumasonyeza kuti chibwenzi chanu sichikuyenda bwino. Dzifunseni kuti, ‘Kodi tingathetse mavutowa mwamtendere?’ Mukadzakwatirana, nonse mudzafunika kukhala ndi luso limeneli.
Mfundo ya m’Baibulo: “Muzikomerana mtima, muzisonyezana chifundo chachikulu komanso muzikhululukirana ndi mtima wonse.”—Aefeso 4:32.
Komabe, ngati mumakhala ndi mikangano ikuluikulu kapenanso pafupipafupi, chimenecho ndi chizindikiro chakuti siinu oyenererana. Ngati zili choncho, ndi bwino kutsimikizira kaye musanakwatirane.
Mfundo yofunika kwambiri: Ngati pali zinthu zina zazikulu zimene mukukayikira zokhudza munthu amene mukufuna kukwatirana naye kapenanso ngati mukuona kuti simunakonzeke kulowa m’banja, musanyalanyaze zinthu zimenezi.
Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu wochenjera akaona tsoka amabisala, koma wosadziwa zinthu amangopitabe ndipo amakumana ndi mavuto.”—Miyambo 22:3.
Ngati mwasankha kuthetsa chibwenzi
Kuthetsa chibwenzi kumawawa. Komabe, ngati pali zinthu zikuluzikulu zimene mmodzi wa inu kapena nonse mukuda nazo nkhawa, ndi nzeru kuthetsa chibwenzicho.
Kodi mungayambire pati? Si bwino kuthetsa chibwenzi polemba meseji kapena imelo. M’malomwake, mungachite bwino kusankha nthawi ndi malo oti mukakambirane za nkhani yaikulu imeneyi.
Mfundo ya m’Baibulo: “Muziuzana zoona.”—Zekariya 8:16.
Kodi kuthetsa chibwenzi ndi chizindikiro chakuti ndinu olephera? Ayi ndithu. Musaiwale kuti kukhala pachibwenzi ndi munthu kungakuthandizeni kuti mudziwane naye bwino n’kusankha kukwatirana naye kapena ayi. Ngakhale pamene chibwenzi chanu chatha, mukhoza kuphunzira zinthu zina pa zimene zakuchitikirani.
Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndaphunzira chiyani zokhudza ineyo pa nthawi imene ndinali pachibwenzi? Kodi zimene zandichitikirazi zandithandiza kuzindikira mbali zina zimene ndiyenera kusintha? Kodi ndi zinthu ziti zimene ndingafunikire kukonza ngati nditasankha kukhalanso pachibwenzi?’
a Kuti mumvetse mmene mavutowa angakhudzire anthu omwe ali pabanja, werengani nkhani yakuti, “Mfundo Zothandiza Mabanja—Zimene Mungachite Ngati Mumakonda Zosiyana” komanso yakuti “Mfundo Zothandiza Mabanja—Muziona Moyenera Zinthu Zimene Zimakukwiyitsani.”