Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 2: N’chifukwa Chiyani Simuyenera Kungokhulupirira Zoti Zinthu Zinachita Kusintha Kuchokera ku Zinthu Zina?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 2: N’chifukwa Chiyani Simuyenera Kungokhulupirira Zoti Zinthu Zinachita Kusintha Kuchokera ku Zinthu Zina?

Alex sakumvetsa. Iye wakhala akukhulupirira kuti kuli Mulungu ndiponso zoti zinthu zinachita kulengedwa. Koma lero aphunzitsi ake a sayansi amaphunzitsa motsimikiza kuti nkhani yakuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina ndi yolondola. Aphunzitsiwo anati asayansi anachita kafukufuku pa nkhaniyi ndipo apeza umboni wodalirika. Alex sakufuna kuoneka ngati wotsalira. Iye akuganizira mumtima mwake kuti, ‘Ngati asayansi atsimikizira kuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, ndiye ine ndine ndani kuti nditsutse zimenezi?’

 Kodi nanunso munakumanapo ndi zinthu ngati zimenezi? Mwina kwa moyo wanu wonse mwakhala mukukhulupirira zimene Baibulo limanena, zoti: “Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Koma mwina posachedwapa anthu ena ayamba kukuuzani zoti sizoona kuti zinthu zinachita kulengedwa koma zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Kodi muyenera kuwakhulupirira?

 Zifukwa ziwiri zimene muyenera kuziganizira mofatsa

  1.   Asayansi sagwirizana chimodzi pa nkhani yakuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Ngakhale kuti kwa nthawi yaitali asayansi akhala akuchita kafukufuku wokhudza nkhaniyi, sanapezebe mfundo zimene onse angagwirizane.

     Zoti muganizire: Ngati asayansi, omwe amati ndi akatswiri, sakugwirizana chimodzi pa nkhaniyi, kodi mukuona kuti n’chinthu chanzeru kumakhulupirira zoti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina?​—Salimo 10:4.

  2.   Muyenera kuganizira mozama zimene mumakhulupirira. Mnyamata wina dzina lake Zachary anati: “Ngati zamoyo zinangokhalako mwangozi, ndiye kuti moyo wathuwu komanso zinthu zonse m’chilengedwechi n’zopanda cholinga.” Zimene Zachary ananena n’zoonadi, chifukwa zikanakhala kuti zinthu zinangosintha kuchokera ku zinthu zina, ndiye kuti moyo ukanakhala wopanda cholinga chilichonse. (1 Akorinto 15:32) Koma ngati zinthu zinachita kulengedwa, ndiye kuti tingapeze mayankho odalirika okhudza moyo komanso tsogolo lathu.​—Yeremiya 29:11.

     Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kudziwa zolondola pa nkhani yakuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina kapena zinachita kulengedwa?​—Aheberi 11:1.

 Mafunso oyenera kuwaganizira

 ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: ‘Zinthu zonse zinangokhalako mwangozi.’

  •   Kodi ndi ndani amene anachititsa kuti zinthu zikhaleko mwangozi?

  •   Kodi ndi mfundo iti pa ziwirizi imene mukuona kuti ndi yomveka; mfundo yakuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina komanso yakuti zinachita kulengedwa?

 ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: ‘Anthu anachita kusanduka kuchokera ku zinyama.’

  •   Ngati anthu anachokeradi ku zinyama monga anyani, n’chifukwa chiyani anthu ndi anzeru kwambiri kuposa anyani? a

  •   N’chifukwa chiyani zinthu zamoyo, ngakhale zing’onozing’ono kwambiri, ndi zogometsa kwabasi? b

 ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: ‘Pali umboni wakuti zamoyo zinangosintha kuchokera ku zinthu zina.’

  •   Kodi munthu amene amanena zimenezi anauona umboniwo?

  •   Kodi ndi anthu angati omwe amangokhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina chifukwa chakuti anamva kuti anthu ophunzira kwambiri amakhulupiriranso zomwezo?

a Anthu ena anganene kuti anthu ndi anzeru chifukwa chakuti ali ndi ubongo waukulu kuposa ubongo wa anyani. Mungapeze zifukwa zokuthandizani kuona kuti maganizo amenewa ndi olakwika, m’kabuku kachingelezi kakuti, The Origin of Life—Five Questions Worth Asking, tsamba 28.