Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Samandilola Kusangalalako?

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Samandilola Kusangalalako?

 Anzanu akonza pate kumapeto kwa mlungu ndipo akuitanirani. Mwapempha makolo anu ngati mungapite nawo kupateko koma akuyankhani kuti “Ayi.” Simukudabwa ndi yankho lawolo chifukwa ulendo wapita anayankhanso chimodzimodzi.

Zimene zili munkhaniyi

 N’chifukwa chiyani nthawi zonse makolo anga sandilola kusangalalako?

 Zikamaoneka kuti nthawi zonse makolo anu amakukanizani mukapempha zinazake, mutha kuganiza kuti safuna kuti muzisangalalako.

 Mtsikana wina dzina lake Marie ankaganiza choncho atangopeza foni. Iye anati: “Bambo anga anandiikira malamulo ambiri okhudza mapulogalamu amene ndingachite dawunilodi pafoni yanga, anthu amene ndiyenera kucheza nawo komanso nthawi imene ndiyenera kusiya kucheza nawo. Koma anzanga ankatha kuchita chilichonse chimene akufuna.”

 Zoti muganizire: Kodi ndi zoona kuti bambo a Marie sankafuna kuti mwana wawo azisangalala? Kodi mwina ankadera nkhawa zinthu ziti?

Zikwangwani zapamsewu zoletsa kupitirira liwiro linalake, zimachepetsa ufulu womwe dalaivala ali nawo koma zimateteza kuti asachite ngozi. N’chimodzimodzinso malamulo amene makolo amakhazikitsa

 Tayesani izi: Yerekezerani kuti inuyo ndinu kholo limene mwana wake wapeza foni kumene. Kodi ndi zinthu ziti zimene inuyo mungade nazo nkhawa? Kodi inuyo mungakhazikitse malamulo otani kuti mumuteteze? Ngati mwana wanu anganene kuti simukufuna kuti azisangalalako, kodi inuyo mungamuyankhe bwanji?

 “Bambo anga ankakonda kundiuza kuti, ‘Uziganizira iweyo uli kholo ngati ineyo.’ Kuganizira zimenezi kunandithandiza kuti ndisamangoona kufunika kwa malamulo amene ankandipatsa koma kuti ndizionanso zifukwa zimene ankaperekera malamulowo. Ndikanakhala kuti ndine kholo, ndikuona kuti ndikanakonda kuti ana anga azitsatira malamulo amene bambo anga amandipatsa.”—Tanya.

 Ndingatani kuti makolo anga azindilolako kuchita zinthu zina?

 Musachite izi: Kukhumudwa, kudandaula kapenanso kukangana nawo.

 “Kulalata sikungathandize chilichonse ndipo khalidwe limeneli lingatopetse inuyo komanso makolo anu. Ngati mungamakangane nawo, makolo anu atha kuona kuti ndinu achibwana ndipo sangakupatseni ufulu wowonjezera.”—Richard.

 M’malo mwake tayesani izi: Muzipewa kuyankha nthawi yomweyo. Koma muziyesa kuona nkhaniyo mmene makolo anu akuionera. Kodi vuto ndi loti sakukhulupirirani inuyo kapena akukayikira malo amene mukupita kapenanso anthu amene akapezeke kumaloko? Bwanji muyese kukambirana nawo nkhaniyo modekha n’cholinga choti mudziwe chifukwa chake akuganiza choncho?

 “Lamulo lililonse limene makolo amapereka amalipereka ndi cholinga chabwino. Sikuti iwo amafuna kuti ndisamasangalale, koma amafuna kuti ndizisangalala m’njira yoti ndisakumane ndi mavuto.”—Ivy.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse, koma wanzeru amakhala wodekha ndipo amalamulira mkwiyo wake.”—Miyambo 29:11.

 Musachite izi: Kuzembera makolo anu.

 Ndinayesera kuphwanya malamulo amene bambo anga anandiikira pa nkhani yogwiritsa ntchito foni. Ndinkayesetsa kupeza njira zotumizirana mameseji ndi anzanga usiku komanso kuchita dawunilodi mapologalamu amene anandiletsa. Koma nthawi zonse ankanditulukira ndipo ankandikhwimitsira malamulo chifukwa choti anasiya kundikhulupirira. Sibwino kupeza njira zophwanyira malamulo amene makoko akhazikitsa.”—Marie.

 M’malo mwake tayesani izi: Muzisonyeza makolo anu kuti mukhoza kugwirizana ndi malamulo amene akhazikitsa, zomwe zingathandize kuti azikukhulupirirani.

 “Muzileza mtima. Zingatenge nthawi kuti makolo anu asinthe lamulo linalake, koma akaona kuti mukumvera malamulo amene anawakhazikitsa, sangavutike kukulolani kuti muzichita zinthu zinanso zambiri.”—Melinda.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Muzimvera makolo anu pa zinthu zonse.”—Akolose 3:20.

 Musachite izi: Kukakamiza makolo anu, mwina powauza zimene ana ena amsinkhu wanu amaloledwa kuchita.

 “Kukakamira zomwe mukufuna sikungathandize kuti zinthu zikuyendereni bwino kapenanso kuti mupeze zomwe mukufunazo.”—Natalie.

 M’malomwake tayesani izi: Gwiritsani ntchito tsamba lakuti “Kuganizira za Malamulo” kuti mukambirane nkhaniyo ndi makolo anu.

 Makolo amafuna kuti aziona kuti ndiwe woganiza bwino. Ndiye ndikamalankhulana ndi makolo anga, ndimawafotokozera zifukwa zomveka bwino osangoti mmene ndikumvera. Ndikamachita zimenezi, nthawi zambiri amandilola kuchita zimene ndapemphazo.”—Joseph.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.”—Aefeso 6:2.