Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi N’zofunikadi Kuti Makolo Azikhazikitsa Malamulo Oti Muzitsatira?

Kodi N’zofunikadi Kuti Makolo Azikhazikitsa Malamulo Oti Muzitsatira?

 Kodi mumaona kuti malamulo ena amene makolo anu anakhazikitsa ndi ovuta? Nkhaniyi komanso tsamba la “Zoti Muchite” zikuthandizani kuti muzitha kulankhula ndi makolo anu pa nkhaniyi.

 Kuona zinthu moyenera

 Maganizo olakwika: Ukangochoka pakhomo ndiye kuti basi, wathana nazo zotsatira malamulo.

 Zoona zake: Munthu akachoka pakhomo sindiye kuti wathana nazo zotsatira malamulo. Umafunikabe kutsatira malamulo a anthu ena monga bwana wako, landilodi wako kapena malamulo a boma. Mtsikana wina wazaka 19 dzina lake Danielle anati: “Ndimaona kuti achinyamata amene satsatira malamulo akakhala pakhomo, amavutika kwambiri akadzayamba kukhala paokha.”

 Baibulo limanena kuti: ‘Muzimvera maboma ndiponso olamulira.’ (Tito 3:1) Mukamatsatira malamulo amene makolo anakuikirani, zimakuthandizani kuti zinthu zizidzakuyenderani bwino mukadzayamba kukhala panokha.

 Zimene mungachite: Muziona kufunika kwa malamulo. Mnyamata wina dzina lake Jeremy anati: “Malamulo amene makolo anga anakhazikitsa ankandithandiza kuti ndizitha kupeza anzanga abwino komanso kugwiritsa ntchito nthawi yanga mwanzeru. Ankandithandizanso kuti ndizichita zinthu zaphindu m’malo mongokhalira kuonera TV komanso kusewera magemu apakompyuta. Zina mwa zinthu zaphinduzo ndimazikondabe mpaka pano.”

 Njira yabwino yofotokozera maganizo anu

 Nanga bwanji ngati lamulo lina likuoneka ngati losamveka? Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Tamara anati: “Nthawi ina makolo anga anandilola kukacheza kudziko lina, koma panopa sandilola kuti ndipite ngakhale kumzinda wina wapafupi kwambiri wongoyenda maminitsi ochepa.”

 Ngati nanunso mukuona kuti malamulo ena ndi osamveka, kodi n’kulakwa kulankhula ndi makolo anuwo? Ayi. Zimangofunika kudziwa nthawi yoyenera komanso mmene mungafotokozere maganizo anuwo.

 Nthawi yoyenera. Mtsikana wina dzina lake Amanda anati: “Mukasonyeza kuti ndinu wokhulupirika pa nkhani yotsatira malamulo a makolo anu, m’pamene mungathe kuwapempha kuti asinthe lamulo linalake.”

 Mtsikana wina dzina lake Daria amaona kuti zimenezi n’zoona. Iye anati: “Mayi anga akaona kuti ndikuyesetsa kutsatira malamulo awo, m’pamene ankatha kusintha malamulo ena.” Muzikumbukira kuti simungauze makolo anu kuti azikukhulupirirani koma zochita zanu n’zimene zingasonyeze ngati angakukhulupirireni kapena ayi.

Kukhala m’nyumba imene ana satsatira malamulo a makolo awo kukhoza kukhala ngati kutera pabwalo la ndege lomwe oyendetsa ndegezo satsatira malamulo awo

 Baibulo limati: “Sunga lamulo la bambo ako, ndipo usasiye malangizo a mayi ako.” (Miyambo 6:20) Mukamatsatira malangizowa, makolo anu adzayamba kukukhulupirirani ndipo mudzatha kuwafotokozera za malamulo omwe mukufuna kuti asinthe.

 Mmene mungalankhulire: Mnyamata wina dzina lake Steven anati: “Munthu amafunika kulankhula mwaulemu komanso modekha ndi makolo ake, osati mwamwano kapena mokalipa.”

 Nayenso Daria ananena kuti: “Ndikakangana ndi mayi anga palibe chimene chinkasintha. Nthawi zina ankangokhwimitsa malamulowo.”

 Baibulo limanena kuti: “Wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse, koma wanzeru amakhala wodekha mpaka pamapeto.” (Miyambo 29:11) Munthu akakhala wodziletsa zinthu zingamuyendere bwino kunyumba kwawo, kusukulu, kuntchito komanso kulikonse.

 Zimene mungachite: Muziyamba mwaganiza kaye musanalankhule. Makolo akhoza kusiya kukukhulupirirani ngati mutangowalankhula kamodzi kokha mutapsa mtima. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti munthu “wosafulumira kukwiya n’ngozindikira zinthu kwambiri.”​—Miyambo 14:29.

 Zimene zingakuthandizeni: Gwiritsani ntchito tsamba la “Zoti Muchite” kuti muganizire bwino za malamulo, ndipo ngati n’zofunika mukambirane ndi makolo anu.