Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingakambirane Bwanji ndi Makolo Anga za Malamulo Amene Anakhazikitsa?

Kodi Ndingakambirane Bwanji ndi Makolo Anga za Malamulo Amene Anakhazikitsa?

 Ndili ndi zaka 15, ndinkaona kuti malamulo amene makolo anga anakhazikitsa anali othandiza, koma popeza ndakwanitsa zaka 19 ndikuona kuti ayenera kundipatsa ufulu wambiri.”​—Sylvia.

 Kodi inunso muli ndi maganizo ngati a Sylvia? Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikuthandizani kuona zimene mungachite kuti mukambirane ndi makolo anu.

 Zimene muyenera kudziwa

 Mungachite bwino kuganizira mfundo zotsatirazi musanakambirane ndi makolo anu za malamulo amene anakhazikitsa:

  •  Popanda malamulo zinthu zikhoza kusokonekera. Kuti timvetse mfundoyi, taganizirani za msewu wokhala ndi magalimoto ambiri. Kodi chingachitike n’chiyani ngati palibe zikwangwani, maloboti komanso malire a liwiro limene munthu angathamange? Malamulo apakhomo amafanana ndi malamulo apamsewu chifukwa amathandiza kuti zinthu zisasokonekere.

  •  Malamulo amasonyeza kuti makolo anu amakukondani. Ngati makolo saika lamulo lililonse zingakhale ngati saganizira mavuto amene mungakumane nawo. Ndiye kodi makolo otero angakhale abwino?

 KODI MUKUDZIWA? Makolo nawonso ali ndi malamulo amene ayenera kutsatira. Ngati mukukayikira, werengani Genesis 2:24; Deuteronomo 6:6, 7; Aefeso 6:4 ndi 1 Timoteyo 5:8.

 Koma kodi mungatani ngati mukuonabe kuti malamulo a makolo anu ndi ovuta kuwatsatira?

 Zimene Mungachite

 Musanakambirane nawo, ganizirani izi: Kodi inuyo mwakhala mukumvera malamulo a makolo anu m’mbuyomu? Ngati yankho ndi lakuti ayi, ndiye kuti si nthawi yabwino yopempha kuti akupatseni ufulu. M’malomwake onani nkhani yakuti, Kodi Ndingatani Kuti Makolo Anga Azindikhulupirira?

 Ngati mwakhala mukuwamvera mukhoza kukonzekera zoti mukambirane ndi makolo anu. Kuyaliratu mfundo zoti mukakambirane nawo kungakuthandizeni kudziwa ngati zimene mukufuna kupempha ndi zoyenera kapena ayi. Kenako mungapemphe makolo anu kuti apeze nthawi komanso malo amene mungakambirane momasuka. Ndiye pamene mukukambirana, muzikumbukira mfundo zotsatirazi:

 Muzikhala aulemu. Baibulo limati: “Mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Choncho muzikumbukira kuti mukakangana kapena kutsutsana nawo, nkhaniyo singathe bwino.

 “Ndikamalemekeza kwambiri makolo anga, nawonso amandilemekeza. Mukamalemekezana, zimakhala zosavuta kuti mugwirizane.”​—Bianca, wazaka 19.

 Muzimvetsera. Baibulo limanena kuti tizikhala ‘ofulumira kumva, odekha polankhula.’ (Yakobo 1:19) Muzikumbukira kuti simuyenera kumangolankhula nokha koma muzikambirana ndi makolo anuwo.

 “Tikamakula tikhoza kuganiza kuti timadziwa zambiri kuposa makolo athu koma zimenezi si zoona. Ndi bwino kutsatira malangizo awo.”​—Devan, wazaka 20.

 Muziganizira mmene akumvera. Muziyesa kuona nkhaniyo mmene makolo anu akuionera. Ndi bwino kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.” Ndiye malinga ndi nkhaniyi, muziganizira zofuna za makolo anu.—Afilipi 2:4.

Kodi njira yabwino yoti mukambirane ndi makolo anu ndi iti?

 Makolo anga ndinkawaona ngati anthu oti ndizikangana nawo osati anzanga. Koma ndazindikira kuti iwo ankaphunzira njira yabwino yosamalira ana ngati mmene inenso ndinkaphunzirira kukhala munthu wodalirika. Zonse zimene ankachita ankazichita chifukwa cha chikondi.”​—Joshua, wazaka 21.

 Muzipereka njira yothetsera mavuto. Tiyerekeze kuti mukufuna kupita kupate inayake ndipo muyendetsa galimoto kwa ola lathunthu. Ndiye makolo anu akukukanizani. Ndi bwino kudziwa zimene zikuwadetsa nkhawa. Kodi ndi kuyendetsako kapena anthu amene muzikacheza nawo?

  •   Ngati vuto ndi kuyendetsako, mukhoza kuwafunsa ngati angalole kuti mupite ndi munthu wina yemwe amayendetsa bwino galimoto.

  •   Koma ngati vuto ndi pate imene ichitike, kodi mungawauze anthu amene akapezekeko komanso amene azikayang’anira zonse n’cholinga choti asamade nkhawa?

 Nthawi zonse muzilankhula mwaulemu komanso kumvetsera bwino zimene makolo anu akunena. Zolankhula komanso zochita zanu zizisonyeza kuti ‘mumalemekeza bambo anu ndi mayi anu.’ (Aefeso 6:2, 3) Kodi makolowo adzasintha maganizo awo? Kaya adzasintha kapena ayi muyenera kutsatira mfundo izi:

 Vomerezani mwaulemu zimene makolo anu asankha. Mfundo imeneyi ndi yofunika koma ambiri saitsatira. Mukayamba kukangana ndi makolo anu chifukwa choti sanalolere maganizo anu, zingachititse kuti mudzavutike kukambirana nawo pa nthawi ina. Koma mukalolera zimene asankha, zingakhale zosavuta kuti akupatseni ufulu pa malamulo ena amene anakhazikitsa.