Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Zimene Mungachite Ngati Simukusangalalanso ndi Sukulu

Zimene Mungachite Ngati Simukusangalalanso ndi Sukulu

 N’zomveka ngati munganene kuti simukonda sukulu, chifukwa kusukulu kukhoza kukhala aphunzitsi okhwimitsa malamulo, anzanu angamakukakamizeni kuchita zinazake, mukhoza kumada nkhawa chifukwa cha mayeso ndiponso mungamakhale ndi mahomuweki ambiri. a Mtsikana wina dzina lake Rachel b anati:

 “Ndingalolere kupita malo ena alionse osati kusukulu. Bola kupita kunyanja, kukacheza ndi anzanga kapenanso kuthandiza makolo anga kuphika ndi kukonza pakhomo.”

 Ngati nanunso mumaona sukulu ngati Rachel, ndiye kuti mukungofunika kupirira mpaka mudzamalize ngati munthu amene ali kundende ndipo akuyembekezera kudzatulutsidwa akamaliza kugwira ukaidi wake. Koma kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti musamaboweke pa nthawi imene muli pasukulu?

 Kodi mukudziwa? Mukakhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya sukulu, simumaionanso ngati ndi yobowa ndipo mumakhala osangalala. Mumayamba kuona kuti sukulu ikukuthandizani kukhala ndi maluso amene angadzakuthandizeni m’tsogolo.

 Kuti muziona sukulu moyenera, tayeserani kuganizira zinthu zotsatirazi:

 Maphunziro anu. Zimene mukuphunzira panopa zidzakuthandizani kuthana ndi mavuto ena amene mungamadzakumane nawo m’tsogolo m’malo momadzadalira anthu ena kuti akuthandizeni. Dzifunseni kuti, ‘Ngakhale kuti pali zinthu zina zokhudza sukulu zimene sizindisangalatsa, kodi ndi zinthu ziti zothandiza zimene ndikuphunzira kusukuluku?’

 Mfundo ya m’Baibulo: “Uteteze nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.”—Miyambo 3:21.

 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti “Ndingatani Ngati Ndimalephera ku Sukulu?

 Makhalidwe anu. Sukulu ingakuthandizeni kudziwa kugwiritsa ntchito nthawi yanu mwanzeru, kukhala munthu wodziletsa komanso kuti muzilimbikira ntchito. Makhalidwe amenewa ndi amene angadzakuthandizeni mukadzakula. Dzifunseni kuti: ‘Kodi sukulu ikundithandiza bwanji kukhala munthu wodziletsa komanso wogwira ntchito mwakhama? Ndingasinthe zinthu ziti kuti ndizichita bwino pa mbali zimenezi?’

 Mfundo ya m’Baibulo: “Kugwira ntchito iliyonse mwakhama kumapindulitsa.”—Miyambo 14:23.

 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti, “Ndingatani Kuti Ndizigawa Bwino Nthawi Yanga?

 Mmene mumachitira zinthu ndi ena. Kuchita zinthu ndi anthu amene mumaphunzira nawo sukulu kungakuthandizeni kuti muyambe kukhala munthu wachifundo komanso waulemu. Mnyamata wina dzina lake Joshua anati: “Kuphunzira kulankhulana ndi anthu n’kofunika ngati mmene kuliri kuphunzira history ndi science. Ndi luso limene mudzaligwiritse ntchito moyo wanu wonse.” Dzifunseni kuti, ‘Kodi kuphunzira sukulu kwandithandiza bwanji kuti ndizichita bwino zinthu ndi ena ngakhale kuti ndimasiyana nawo kochokera komanso zikhulupiriro?’

 Mfundo ya m’Baibulo: “Muziyesetsa kukhala mwamtendere ndi anthu onse.”​—Aheberi 12:14.

 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti, “Kodi Ndingakulitse Bwanji Luso Lolankhulana Ndi Anthu?

 Tsogolo lanu. Sukulu ingakuthandizeni kuzindikira maluso amene muli nawo zomwe zingakuchititseni kukhala ndi zolinga zogwirizana ndi maluso anuwo. Mtsikana wina dzina lake Brooke anati: “Mwina mukhoza kuphunzira ntchito inayake ngati mmene ine ndinachitira n’cholinga choti mukadzamaliza sukulu musadzavutike kupeza ntchito.” Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikadzamaliza sukulu ndizidzachita zotani kuti ndizidzapeza zofunika pa moyo? Kodi ndingaphunzire zinthu ziti kuti ndidzakwanitse kugwira ntchitoyo?’

 Mfundo ya m’Baibulo: “Dziwa kumene ukupita.”​—Miyambo 4:26, Contemporary English Version.

a Mfundo zambiri zimene zafotokozedwa munkhaniyi zingathandizenso achinyamata omwe amaphunzira sukulu panyumba.

b Mayina ena asinthidwa.