ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Ndingatani Ngati Ndili Ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?
“Zaka zapitazo, ndinkalimbana ndi nkhawa kwambiri moti zinkangokhala ngati kuti tsiku lililonse ndili pa chintchito chothimitsa moto. Nthawi imeneyo ndinkangoganizira zodzipha. Sikuti ndinkafunadi kufa, koma ndinkangofuna kuthana ndi mavuto omwe ndinkakumana nawo.”—Jonathan, wazaka 17.
Pa kafukufuku wina amene anachitidwa pa achinyamata 14,000 a kukoleji, pafupifupi wachinyamata mmodzi pa 5 aliwonse anavomera kuti anaganizapo zofuna kudzipha. a Kodi mungatani ngati nanunso mumaona kuti bola kungodzipha?
Dekhani. Tsimikizani mtima kuti simudzachita zinthu mopupuluma. Ngakhale kuti ndi zoona kuti mavuto omwe mukukumana nawo angaoneke aakulu kwambiri, pali njira zomwe mungatsatire kuti muthane nawo.
Mukhoza kumaganiza kuti palibenso zomwe mungachite ndi mavuto omwe mukukumana nawo. Koma si nthawi zonse pomwe zomwe timaganiza zimakhaladi zolondola. Njira zothanirana ndi mavuto anu zilipo, ndipo ngati mutapeza thandizo loyenera, zinthu zikhoza kuyamba kuyenda bwino mwamsanga kuposanso mmene mukuganizira.
Mfundo ya m’Baibulo: “Timapanikizidwa mwamtundu uliwonse, koma osati kupsinjidwa moti n’kulephera kusuntha. Timathedwa nzeru, koma osati mochita kusoweratu pothawira.”—2 Akorinto 4:8.
Zomwe mungachite: Ngati mukumangoganizira zodzipha, gwiritsani ntchito njira zomwe zilipo kuti mupeze thandizo. Mwachitsanzo, mungaimbire achipatala. Ogwira ntchito zachipatala, anaphunzitsidwa ndi cholinga choti akuthandizeni ndipo ndi ofunitsitsa kukuthandizani.
Lankhulani ndi winawake. Pali anthu omwe amakukondani omwenso ndi ofunitsitsa kukuthandizani. Anthuwa ndi monga anzanu komanso achibale anu omwe pawokha sangadziwe zomwe mukukumana nazo pokhapokha mutawauza.
Anthu ena amaona zinthu bwinobwino akavala magalasi. Anthu ena nawonso angakuthandizeni kuti muyambe kuona zinthu moyenera komanso kuti musinthe maganizo n’kuyamba kuona moyo wanu kukhala wofunika.
Mfundo ya m’Baibulo: “Bwenzi lenileni . . . ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.
Zomwe mungachite: Kuti muyambe kukambirana, munganene kuti: “Masiku amenewa ndikumavutika maganizo ndi zinazake. Mungakonde kuti ndikuuzeni?” Kapena mukhoza kunena kuti: “Ndikulimbana ndi mavuto enaake omwe ndikuona kuti sindingathe kuthana nawo pa ndekha. Mungandithandizeko?”
Kaonaneni ndi adokotala. Matenda a nkhawa kapena ovutika maganizo akhoza kuchititsa munthu kuona kuti palibenso chifukwa chokhalira ndi moyo. Koma chosangalatsa n’chakuti mankhwala a matenda amenewa alipo.
Monga mmene chimfine chimachititsira kuti munthu asakhale ndi chilakolako chofuna kudya, matenda ovutika maganizo amachititsanso munthu kuti asamasangalale ndi moyo. Komabe, matenda onsewa ali ndi mankhwala ake.
Mfundo ya m’Baibulo: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”—Mateyu 9:12.
Zomwe mungachite: Muzigona mokwanira, kuchita masewera olimbitsa thupi komanso kudya chakudya chopatsa thanzi. Ngati thupi lanu si lathanzi, zingakhalenso zovuta kuti muziganiza bwino.
Muzipemphera. Baibulo limanena kuti Mlengi wathu “ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yohane 3:20) Pezani mpata woti mupemphere kwa iye. Popempherapo, tchulani dzina lake lakuti Yehova ndipo muuzeni zonse zomwe zili mumtima mwanu.
Mavuto ena ali ngati chikatundu cholemera chomwe simungathe kunyamula nokha. Mulungu wanu Yehova, ndi wokonzeka kuti akuthandizeni.
Mfundo ya m’Baibulo: “Zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afilipi 4:6, 7.
Zomwe mungachite: Kuwonjezera pa kuuza Yehova za mavuto anu, tayesani kuganizira chinthu chimodzi chabwino chomwe mungamuthokoze nacho. (Akolose 3:15) Kukhala ndi mtima woyamikira, kungakuthandizeni kuti muziganizira zinthu zabwino ndipo zimenezi zingakuthandizeni kukhala ndi chiyembekezo.
Mukayamba kuona kuti moyo ulibenso phindu, ndi bwino kupempha ena kuti akuthandizeni. Zimenezi ndi zomwe Jonathan amene tamutchula kumayambiriro kwa nkhaniyi anachita. Iye ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkakambirana ndi makolo anga komanso ndinapita kuchipatala kukalandira chithandizo. Koma panopo ndikupezako bwino. Ngakhale kuti nthawi zina ndimakhumudwabe ndi zinthu zina, sindikhalanso ndi maganizo ofuna kudzipha.”
a Kafukufukuyu anachitika mu 2019 ndi a U.S. Centers for Disease Control and Prevention.