Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Anzanu

Kupeza anzako apamtima kungakhale kovuta, koma kupitiriza kukhala nawo kungakhalenso kovuta kwambiri. Mungatani kuti mupeze komanso mupitirize kukhala ndi anzanu abwino?

Kupeza Anzanu Komanso Kupitiriza kugwirizana Nawo

Kodi Mnzako Weniweni Ungamudziwe Bwanji?

N’zosavuta kupeza anzanu amene sangakuthandizeni, koma kodi mungapeze bwanji mnzanu weniweni?

Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi Anzanu Apamtima?

Mfundo 4 zomwe zingakuthandizeni kuti mupeze anzanu apamtima.

N’chifukwa Chiyani Anzanga Sandikonda?

Si inu nokha amene mukusowa wocheza naye kapena amene mulibe mnzanu. Werengani nkhaniyi kuti muone mmene anthu ena athetsera vutoli.

Kodi Mungatani Ngati Mumasowa Wocheza Naye

Kusowa ocheza nawo kwa nthawi yaitali kumasokoneza thanzi la munthu mofanana ndi mmene zimakhalira ndi munthu yemwe amasuta ndudu 15 pa tsiku. Kodi mungatani ngati nthawi zina mumaona kuti mumangokhala nokhanokha ndipo mukusowa wocheza naye?

Kulimbana ndi Vuto Losowa Ocheza Nawo

Kodi mumasowa anthu ocheza nawo? Gwiritsani ntchito mafunsowa kuti mudziwe chimene chimapangitsa kuti muzisowa anthu ocheza nawo komanso zimene mungachite kuti muthane ndi vutoli.

Mungatani Kuti Musamachite Manyazi Kwambiri?

Zinthu zisamakupiteni ndipo mukhoza kupeza anzanu ambiri.

Zimene Mungachite Kuti Mupeze Anzanu Odalirika

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chimene chinathandiza Davide kukhala mnzake wapamtima wa Yonatani.

Kodi Ndiwonjezere Anzanga?

Zimakhala bwino kukhala ndi kagulu kochepa ka anzanu, koma sikuti zimenezi zimathandiza nthawi zonse. N’chifukwa chiyani?

Kuonjezera Anzanga

Onani zimene mungachite kuti muthe kuonjezera anzanu komanso chifukwa chake.

Kodi Ndi Mnzanga Chabe Kapena Amandifuna?—Gawo 2: Kodi Ndikumukopa?

Kodi mnzanuyu angaganize kuti mukumufuna chibwenzi? Zimene zingakuthandizeni.

Musamapitirire Malire

Muzitumiza mameseji oyenera kwa anzanu amene si amuna kapena akazi anu.

Mavuto

Ndingatani Ngati Mnzanga Atandikhumudwitsa?

Muzikumbukira kuti tonse timakhumudwitsa anzathu. Koma kodi mungatani ngati mnzanu atalankhula kapena kuchita zinthu zomwe zakukhumudwitsani?

Moyo Wanga Wachinyamata—Kodi Ndingapewe Bwanji Kutengera Zochita za Anzanga?

Onani mmene mfundo za m’Baibulo zingakuthandizireni kuti mukwanitse kulimbana ndi vutoli.

Kodi Mungatani Kuti Musamangotengera Zochita za Anzanu?

Munthu akhoza kuyamba kuchita zoipa chifukwa chotengera zochita za anzake. Zimene muyenera kudziwa zokhudza kutengera zochita za anzanu komanso zimene mungachite pothetsa vutoli.

Musamangotengera Zochita za Anzanu

Zinthu 4 zimene zingakuthandizeni kuti muzisankha nokha zochita mwanzeru.

Ndingatani Ngati Anzanga Amandiona Kuti Ndine Wotsalira?

Kodi mumaona kuti n’zoyenera kuchita zinthu kuti mufanane ndi anzanu omwe satsatira mfundo za makhalidwe abwino kapena mumaona kuti chofunika ndi kungokhala mmene mulili?

Kodi Ndingakulitse Bwanji Luso Lolankhulana Ndi Anthu?

Mfundo zitatu zimene zingakuthandizeni kuti musamavutike kuyamba kulakhulana ndi anthu.

N’chifukwa Chiyani Ndimangolankhula Zolakwika?

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muziganiza musanalankhule?

Ndingatani Kuti Ndikonze Zomwe Ndinalakwitsa M’mbuyo?

Musaganize kuti kukonza zomwe munalakwitsa n’kovuta kwambiri.

Kodi Ndingatani Ngati Anthu Ena Akukonda Kunena za Ine?

Kodi mungatani kuti zinthu zabodza zimene anthu akufalitsa zokhudza inuyo zisawononge mbiri yanu?

Kodi Ndingatani Kuti Ndithetse Miseche?

Ngati anzanu ayamba kulankhula zonyoza kapena zoipa za anthu ena, musayankhire nawo koma sinthani nkhaniyo!

Kodi Kukopana Kuli Ndi Vuto?

Kodi kukopana n’kutani? N’chifukwa chiyani anthu ena amakopana? Kodi kukopana kuli ndi vuto?

Kodi N’kungocheza Kapena Kukopana?

Nkhani imene munthu wina angaione ngati yocheza, wina angaione ngati yomukopa. Mungatani kuti muzipewa kutumiza mameseji olakwika?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Mameseji a Pafoni?

Mameseji a pafoni akhoza kuononga ubwenzi wanu ndi anzanu komanso mbiri yanu. Werengani kuti mudziwe mmene zimenezi zingachitikire

Kodi Mungasonyeze Bwanji Khalidwe Labwino Mukamatumiza ndi Kulandira Mameseji pa Foni?

Kodi mukuona kuti n’kupanda ulemu kusiya kaye kucheza ndi mnzanu kuti muwerenge meseji? Kapena mukuganiza si bwino kumangopitirizabe kucheza ndi mnzanuyo osawerenga kaye meseji imene mwalandira?