Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Banja

Kodi zikukuvutani kugwirizana ndi makolo anu? Kodi simumagwirizana kwenikweni ndi abale anu? Baibulo lingakuthandizeni kuthana ndi mavuto amenewa komanso mavuto ena amene mabanja amakumana nawo.

Kuchita Zinthu ndi Makolo

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwirizana ndi Makolo Anga?

Onani zinthu 5 zimene mungachite kuti musamakangane ndi makolo anu.

Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhulana Bwino ndi Makolo Anga?

Pali zabwino zambiri zimene mungapeze chifukwa cholankhulana bwino ndi makolo anu.

Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhulana Bwino ndi Makolo Anga?

Kodi mungatani kuti mulankhulane ndi makolo anu pamene mukuona ngati simufuna kulankhula?

Kodi Ndingakambirane Bwanji ndi Makolo Anga za Malamulo Amene Anakhazikitsa?

Mukamalankhula mwaulemu ndi makolo anu zinthu zingakuyendereni bwino.

Kodi N’zofunikadi Kuti Makolo Azikhazikitsa Malamulo Oti Muzitsatira?

Kodi mumaona kuti malamulo amene makolo anu anakhazikitsa ndi ovuta? M’nkhaniyi muli mfundo zimene zingakuthandizeni kuti muzitha kuona malamulowo moyenera.

Kuganizira za Malamulo

Ganizirani bwino za malamulo omwe mumaona kuti ndi ovuta.

Kodi Ndingatani Kuti Ndizilankhulana Bwino ndi Makolo Anga?

Mfundo zimene zili m’nkhaniyi zingakuthandizeni kuti muzilankhulana bwino ndi makolo anu

Kodi Ndingatani Ngati Sindinamvere Lamulo la Makolo Anga??

Simungasinthe zimene zachitika koma mungathandize kuti zinthu zisaipe kwambiri. Nkhaniyi ikufotokoza zimene mungachite.

Kodi Ndingatani Kuti Makolo Anga Azindikhulupirira?

Kuphunzira kukhala wodalirika ndi kofunika kwa aliyense osati kwa achinyamata okha.

Kodi Ndingatani Kuti Makolo Anga Azindilolako Kuchita Zinthu Zina?

Mukhoza kuganiza kuti makolo anu akuyenera kumakuonani kuti ndinu munthu wamkulu, koma iwo sangagwirizane ndi maganizo amenewa. Kodi mungachite zinthu ziti kuti makolo anu ayambe kukukhulupirirani?

Kodi Mumaona Kuti Makolo Anu Sangakuloleni Kupita Kokasangalala?

Kodi ndingozemba n’kupita kokasangalala, kapena ndipemphe makolo anga?

Kodi Ndingatani Ngati Bambo Kapena Mayi Anga Atayamba Kudwala?

Si inu nokha amene mukukumana ndi vuto limeneli. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene atsikana ena awiri anachita kuti athe kupirira.

Ngati Bambo Kapena Mayi Anu Akudwala

Mfundo za patsambali zingakuthandizeni posamalira bambo kapena mayi anu amene akudwala matenda aakulu komanso podzisamalira nokha.

Kodi Makolo Anu Akufuna Kuthetsa Banja Lawo?

Kodi mungatani kuti musamangokhala wokhumudwa kapena wokwiya?

Moyo wa Panyumba

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kukhala Mwamtendere ndi Abale Anga?

Ngakhale kuti mumakonda abale anu, koma nthawi zina mukhoza kuwakhumudwitsa.

Zimene Mungachite Mukasemphana Maganizo ndi Abale Anu

Gwiritsani ntchito tsambali kuti mumvetse bwino zimene zachitika komanso kuti muyambirenso kugwirizana ndi abale anu.

Kodi Ndingatani Kuti Ndizikhala ndi Mpata Womachita Zinthu Pandekha?

Kodi mumaona kuti makolo anu akukulondalondani? Nanga mungatani kuti vuto limeneli lichepe?

Kodi Nthawi Zina Mumasowa Mpata Wochitira Zinthu Panokha?

Onani zimene mungachite kuti makolo anu azikudalirani.

Kodi Ndafika Poti Nditha Kuchoka Pakhomo pa Makolo Anga?

Kodi mungadzifunse mafunso ati musanaganize zoti musamuke?

Kodi Mukufuna Kubwereranso Kunyumba?

Kodi zinthu zakuvutani ndipo mukuona kuti mukufunikanso kubwerera kwanu? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zomwe zingakuthandizeni kuti zinthu ziyambenso kukuyenderani bwino.