Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Maluso Othandiza pa Moyo

Onani maluso komanso makhalidwe ofunika kwambiri omwe muyenera kukhala nawo kuti adzakuthandizeni mukadzakula.

Kudziletsa pa Nkhani ya Mmene Mumamvera

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamasinthesinthe Mmene Ndimamvera?

Anthu ambiri amasinthasintha mmene akumvera, koma zimenezi zimasokoneza ana ambiri. Koma chosangalatsa n’choti utha kudziwa bwino zimene zikukuchitikira komanso n’zotheka kupirira vutoli.

Kulimbana ndi Vuto la Mmene Mukumvera Mumtima

Zoti muchitezi zikuthandizani kuti mudziwe zimene mungachite mukamakumana ndi mavuto.

Zimene Mungachite Kuti Muyambirenso Kusangalala

Kodi mungatani ngati mukukhalabe okhumudwa kwa nthawi yaitali?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangoganizira Zinthu Zolakwika?

Mukhoza kumaganizira zinthu zabwino mukamatsatira mfundo zomwe zili mu nkhaniyi.

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamapse Mtima?

Pali malemba 5 amene angakuthandizeni kuti musamapse mtima wina akakuyambani.

Kodi Mungatani Kuti Muziugwira Mtima?

Mfundo 5 zokuthandizani kuti muziugwira mtima.

N’chiyani Chingandithandize Ndikakhala Ndi Nkhawa?

Zinthu 5 zimene zingakuthandizeni kuti muzida nkhawa pa zinthu zoyenera m’malo mwa zinthu zimene zingakubweretserani mavuto.

Kodi N’chiyani Chingandithandize Ndikakumana ndi Mavuto?

Achinyamata akufotokoza zimene anachita atakumana ndi mavuto.

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamagonje Poyesedwa?

Onani zinthu zitatu zimene zingakuthandizeni kuti musamagonje mukayesedwa.

Mungatani Kuti Musamagonje Mukakumana ndi Mayesero?

Mwamuna komanso mkazi weniweni amatha kupewa mayesero. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu 6 zimene zingakuthandizeni kusagonja mukamayesedwa komanso kuti musakhale ndi nkhawa chifukwa chodziwa kuti mwagonja.

Nthawi Komanso Ndalama

Ndingatani Kuti Ndizigawa Bwino Nthawi Yanga?

Mfundo 5 zomwe zingakuthandizeni kuti muzipewa kuwononga nthawi yanu.

Kodi Ineyo Ndingatani Kuti Ndipewe Vuto la Kupanikizika?

Kodi n’chiyani chimayambitsa vuto la kupanikizika? Kodi inunso mumapanikizika kwambiri? Ngati ndi choncho, kodi mungatani kuti muthane ndi vutoli?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamachite Zinthu Mozengereza?

Werengani malangizo amene angakuthandizeni kuti musamachite zinthu mozengereza

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamawononge Ndalama?

Kodi nthawi ina munapitapo mu shopu kuti mukangoona zinthu koma n’kugula chinthu chodula kwambiri? Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikuthandizani.

Zimene Mungachite Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama

Gwiritsani ntchito zoti muchitezi kuti muone kuchuluka kwa zinthu zofunika ndi zongowonjezera komanso onani ngati zonse zikugwirizana ndi bajeti yanu.

Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama Zanu?

Muzisunga bwino ndalama zanu kuti zidzakuthanizeni mukadzafuna kuzigwiritsa ntchito.

Kukula

Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?

Aliyense amalakwitsa koma si onse amene amaphunzirapo kanthu.

Zimene Mungachite Mukalakwitsa Zinthu

Mafunso a patsambali angakuthandizeni kudziwa zimene mungachite mukalakwitsa zinthu.

Kodi Ndizitani Munthu Wina Akandidzudzula?

Achinyamata ena amakhala ngati tambula yagalasi yomwe sichedwa kusweka moti akangodzudzulidwa ngakhale pa zinthu zazing’ono, amakwiya kwambiri. Kodi inunso mumatero?

Kodi Mumatani Wina Akakupatsani Malangizo pa Zomwe Mwalakwitsa?

Kodi zingatheke bwanji kuti malangizo owawa kwambiri akhale othandiza kwambiri?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kukhala Oona Mtima?

Kodi mumafunika kunama kuti zinthu zikuyendereni bwino? Onani chifukwa chake kuchita zinthu moona mtima n’kothandiza kwambiri.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupewa Kunama ndiponso Kuba?

Kodi si zoona kuti anthu achinyengo zinthu zimawayendera bwino?

Kodi Ndinu Woona Mtima?

Dzifufuzeni pogwiritsa ntchito mafunso atatuwa.

Zimene Mungachite Zinthu Zikasintha

Zinthu zimasintha pamoyo. Onani zimene ena achita kuti azolowere zinthu zitawasinthira.

Kodi Ndine Munthu Wodalirika?

Achinyamata ena amapatsidwa ufulu wambiri poyerekezera ndi anzawo ena. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti pakhale kusiyana kotereku?

Kodi Ndine Wopirira?

Aliyense amakumana ndi mavuto, choncho m’pofunika kuphunzira kukhala wopirira, ngakhale mavutowo atakhala aang’ono kapena aakulu.

Kodi Ndingatani Kuti Maganizo Anga Azikhala pa Zimene Ndikupanga?

Taganizirani njira zitatu zosonyeza mmene zipangizo zamakono zingakusokonezereni ndipo onani zimene mungachite kuti muzikwanitsa kuika maganizo anu pa chinthu chimodzi.

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Chinenero China?

Kodi pamakhala mavuto otani? Nanga pamakhala mapindu otani?

Zimene Zingakuthandizeni Kuphunzira Chinenero China

Kuphunzira chinenero china kumafunika kuyeserera, nthawi ndi khama. Zoti muchitezi zikuthandizani kudziwa zoyenera kuchita pophunzira chinenero china.

Kodi Ndafika Poti Nditha Kuchoka Pakhomo pa Makolo Anga?

Kodi mungadzifunse mafunso ati musanaganize zoti musamuke?

Kodi Mukufuna Kubwereranso Kunyumba?

Kodi zinthu zakuvutani ndipo mukuona kuti mukufunikanso kubwerera kwanu? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zomwe zingakuthandizeni kuti zinthu ziyambenso kukuyenderani bwino.

Kuchita Zinthu ndi Anthu Ena

Mungatani Kuti Musamachite Manyazi Kwambiri?

Zinthu zisamakupiteni ndipo mukhoza kupeza anzanu ambiri.

Ndingatani Ngati Anzanga Amandiona Kuti Ndine Wotsalira?

Kodi mumaona kuti n’zoyenera kuchita zinthu kuti mufanane ndi anzanu omwe satsatira mfundo za makhalidwe abwino kapena mumaona kuti chofunika ndi kungokhala mmene mulili?

Kodi Ndingakulitse Bwanji Luso Lolankhulana Ndi Anthu?

Mfundo zitatu zimene zingakuthandizeni kuti musamavutike kuyamba kulakhulana ndi anthu.

Kodi Kukhala ndi Ulemu N’kofunikadi?

Kodi ulemu ndi wofunika masiku ano, kapena ndi nkhani yachikale?

N’chifukwa Chiyani Ndimangolankhula Zolakwika?

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muziganiza musanalankhule?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupepesa?

Onani zifukwa zitatu zimene muyenera kupepesera ngakhale pamene mukuona kuti simunalakwe chilichonse.

N’chifukwa Chiyani Ndikufunika Kumathandiza Ena?

Kuchitira ena zabwino kumakuthandizani m’njira ziwiri. Kodi njira zimenezi ndi zotani?

Zimene Mungachite Kuti Muthandize Ena

Mukhoza kuthandiza anthu amene mumakhala nawo pafupi. Nkhani ino ili ndi njira zitatu zimene mungatsatire pokonza mapulani oti muthandize ena.

Kodi Ndingatani Ngati Anthu Ena Akukonda Kunena za Ine?

Kodi mungatani kuti zinthu zabodza zimene anthu akufalitsa zokhudza inuyo zisawononge mbiri yanu?

Ndingatani Ngati Mnzanga Atandikhumudwitsa?

Muzikumbukira kuti tonse timakhumudwitsa anzathu. Koma kodi mungatani ngati mnzanu atalankhula kapena kuchita zinthu zomwe zakukhumudwitsani?

Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?

Anthu ambiri amene akuvutitsidwa amaona kuti palibe chimene angachite. Nkhaniyi ikufotokoza zimene mungachite kuti anthu asiye kukuvutitsani.

Ndingatani Ngati Anzanga Amandivutitsa?

Simungathe kuchititsa kuti anthu asamakuvutitseni, koma mungathe kusintha mmene mumawayankhira.

Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani?

Onerani vidiyoyi kuti mudziwe chifukwa chake anthu amavutitsa anzawo komanso zimene mungachite kuti asiye kukuvutitsani.