Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Moyo Wauzimu

Nthawi zina sizikhala zophweka kutsatira mfundo za m’Baibulo, koma kuzitsatira kumathandiza kuti zinthu zizikuyenderani bwino pa moyo wanu. Kodi zimenezi zingatheke bwanji?

Kukhulupirira Mulungu

Achinyamata Ena Akufotokoza Zokhudza Kukhulupirira Kuti Kuli Mulungu

M’vidiyo ya maminitsi atatuyi, achinyamata akufotokoza chifukwa chake amakhulupirira kuti kuli Mulungu.

Kodi N’zomveka Kukhulupirira Kuti Mulungu Alipo?

Onani achinyamata awiri amene anapeza mayankho a mafunso awo n’kulimbitsa chikhulupiriro chawo.

Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 1: N’chifukwa Chiyani Ndimakhulupirira Kuti Kuli Mulungu?

Kodi mungakonde kuti muzifotokozera ena molimba mtima zimene mumakhulupirira zoti kuli Mulungu? Werengani nkhaniyi kuti mupeze mfundo zimene zingakuthandizeni kuyankha ngati munthu wina wakufunsani zimene mumakhulupirira.

Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 3: N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kukhulupirira Kuti Zinthu Zinachita Kulengedwa?

Kodi munthu amafunika kudana ndi sayansi n’cholinga choti azikhulupirira zoti zinthu zinachita kulengedwa?

Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 4: Kodi Ndingafotokozere Bwanji Munthu Kuti Zinthu Zinachita Kulengedwa?

Simukufunika kuchita kukhala wodziwa kwambiri sayansi kuti muthe kufotokozera munthu umboni wosonyeza kuti n’zomveka kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa. Gwiritsirani ntchito zitsanzo zosavuta kumva zopezeka m’Baibulo.

N’chifukwa Chiyani Ndimakhulupirira Zoti Kuli Mulungu?

Khalani okonzeka kuti muzitha kufotokoza zimene mumakhulupirira koma mwaulemu, mopanda mantha komanso mosadandaula.

Zimene Mungachite Kuti Mukhale pa Ubwenzi ndi Mulungu

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupemphera?

Kodi pemphero limangothandiza kuti maganizo akhale m’malo, kapena limathandizanso m’njira zina?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupezeka Pamisonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu?

Mlungu uliwonse a Mboni za Yehova amakumana kawiri pa nyumba yomwe amalambirira yotchedwa Nyumba ya Ufumu. Kodi kumeneko kumachitika zotani, nanga mungapindule bwanji ngati mutapezeka pamisonkhano yawo?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kukhala Moyo Wachiphamaso?

Njira 4 zomwe zingakuthandizeni kuti musiye kukhala moyo wachinyengowu.

Zimene Mungaphunzire kwa Anthu Otchulidwa M'Baibulo

Muziyamikira Zinthu Zopatulika

Kodi inuyo mungachite zinthu ziti kuti musonyeze kuti mumayamikira zinthu zopatulika?

Muzilandira Uphungu Modzichepetsa

Kodi mungaphunzirepo chiyani mukaganizira mmene Natani anaperekera uphungu kwa Davide?

Tetezani Kulambira Koona

Kodi ndi mbali ziti pa moyo wanu zimene mungafunikire kusonyeza kulimba mtima kuti muteteze kulambira koona?

Mulungu Anachiritsa Hezekiya

Werengani nkhani ya m’Baibuloyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti mapemphero anu azikhala abwino.

Anapulumutsidwa Mung’anjo Yamoto

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene kukhalabe olimba pa zimene mumakhulupirira kulili kofunika.

Mulungu Anayankha Pemphero la Nehemiya

Phunzirani za Nehemiya ndipo onani mmene Mulungu anamuthandizira polimbana ndi adani.

Tsanzirani Msamariya Wachifundo

Werengani fanizo la Msamariya wachifundo ndipo muliganizire mozama kuti muone zimene mungaphunzirepo.

Kuwerenga Ndiponso Kuphunzira Baibulo

Achinyamata Akukambirana Zokhudza Kuwerenga Baibulo

Kuwerenga sikophweka, koma kuwerenga Baibulo n’kothandiza kwambiri. Achinyamata anayi akufotokoza mmene kuwerenga Baibulo kwawathandizira.

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?

Yankho la funso limeneli lingakuthandizeni kuti muzisangalala kwambiri pa moyo wanu.

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 1: Kuganizira Mozama Mfundo za M’baibulo

Tiyerekeze kuti mwaona chikwama cha ndalama chomwe chikuoneka kuti ndi chakalekale, kodi simungakhale ndi chidwi kuti muone zimene zili mkatimo? Baibulo lili ngati chikwama choterocho. Mumapezeka mfundo zambiri zothandiza.

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 2: Zimene Mungachite Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikusangalatsani

Zinthu 5 zomwe zingakuthandizeni kuti muziona zimene mukuwerenga m’Baibulo kuti ndi zenizeni.

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 3: Zimene Mungachite Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikuthandizani Kwambiri

Mfundo 4 zomwe zingakuthandizeni kuti kuwerenga Baibulo kuzikuthandizani kwambiri

Kukula Mwauzimu

Kodi Ndingaphunzitse Bwanji Chikumbumtima Changa?

Chikumbumtima chanu chimasonyeza kuti ndinu munthu wotani. Chimasonyezanso mfundo zimene mumakhulupirira. Ndiye kodi chikumbumtima chanu chimasonyeza zotani zokhudza inuyo?

Ndingatani Kuti Ndikonze Zomwe Ndinalakwitsa M’mbuyo?

Musaganize kuti kukonza zomwe munalakwitsa n’kovuta kwambiri.

Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 1: Tanthauzo la Kubatizidwa

Ngati mukuganiza zobatizidwa, poyamba muyenera kumvetsa tanthauzo lake.

Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?—Gawo 2: Kukonzekera Kubatizidwa

Yankhani mafunsowa kuti muone ngati mwakonzeka kubatizidwa.

Kodi Ndiyenera Kuchita Chiyani Ndikabatizidwa?—Mbali Yoyamba: Pitirizani Kuchita Zinthu Zofunika

Pambuyo pobatizidwa, pitirizani kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu. Pitirizani kuphunzira Baibulo, kupemphera, kuuza ena zomwe mumakhulupirira komanso kupezeka pamisonkhano yachikhristu.

Cameron Anapeza Moyo Wabwino Kwambiri

Kodi mukufuna kukhala munthu wosangalala? Mvetserani pamene Cameron akufotokoza zimene zinamuthandiza kuti akhale wosangalala atapita kumalo amene samaganizira kuti angafikeko.