Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mtendere wa M’maganizo

Achinyamata ambiri amavutika ndi nkhawa, matenda amaganizo, kudziona kuti ali okhaokha ndiponso amatopa kwambiri. Onani zimene zingakuthandizeni kukhala ndi mtendere wa m’maganizo.

Kuvutika ndi Maganizo Oipa

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamasinthesinthe Mmene Ndimamvera?

Anthu ambiri amasinthasintha mmene akumvera, koma zimenezi zimasokoneza ana ambiri. Koma chosangalatsa n’choti utha kudziwa bwino zimene zikukuchitikira komanso n’zotheka kupirira vutoli.

Kulimbana ndi Vuto la Mmene Mukumvera Mumtima

Zoti muchitezi zikuthandizani kuti mudziwe zimene mungachite mukamakumana ndi mavuto.

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangoganizira Zinthu Zolakwika?

Mukhoza kumaganizira zinthu zabwino mukamatsatira mfundo zomwe zili mu nkhaniyi.

Kodi Ndingatani Ngati Ndili ndi Matenda Ovutika Maganizo?

Mfundo zomwe zili m’nkhaniyi zingakuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti muchire.

Zimene Mungachite Mukakhumudwa

Kodi n’chiyani chimene chingakuthandizeni kukhala wosangalala mukakhumudwa?

Zimene Mungachite Kuti Muyambirenso Kusangalala

Kodi mungatani ngati mukukhalabe okhumudwa kwa nthawi yaitali?

Kodi Mungatani Ngati Mumasowa Wocheza Naye

Kusowa ocheza nawo kwa nthawi yaitali kumasokoneza thanzi la munthu mofanana ndi mmene zimakhalira ndi munthu yemwe amasuta ndudu 15 pa tsiku. Kodi mungatani ngati nthawi zina mumaona kuti mumangokhala nokhanokha ndipo mukusowa wocheza naye?

N’chiyani Chingandithandize Ndikakhala Ndi Nkhawa?

Zinthu 5 zimene zingakuthandizeni kuti muzida nkhawa pa zinthu zoyenera m’malo mwa zinthu zimene zingakubweretserani mavuto.

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamapse Mtima?

Pali malemba 5 amene angakuthandizeni kuti musamapse mtima wina akakuyambani.

Kodi Mungatani Kuti Muziugwira Mtima?

Mfundo 5 zokuthandizani kuti muziugwira mtima.

Kodi Ndimafuna Kuti Ndisamalakwitse Chilichonse?

Kodi mungasiyanitse bwanji pakati pa kuyesetsa kuchita bwino ndi kuyesa kuchita zinthu zosatheka?

Zomwe Zingakuthandize Kuti Usamayembekezere Kuchita Zinthu Mosalakwitsa Chilichonse

Zoti muchitezi zikuthandizani kukhala ndi maganizo oyenera a zimene anthu ena komanso inuyo mungakwanitse kuchita.

Mavuto

Zimene Mungachite Zinthu Zikasintha

Zinthu zimasintha pamoyo. Onani zimene ena achita kuti azolowere zinthu zitawasinthira.

Kodi Ndine Wopirira?

Aliyense amakumana ndi mavuto, choncho m’pofunika kuphunzira kukhala wopirira, ngakhale mavutowo atakhala aang’ono kapena aakulu.

Kodi N’chiyani Chingandithandize Ndikakumana ndi Mavuto?

Achinyamata akufotokoza zimene anachita atakumana ndi mavuto.

Mungatani Ngati Muli ndi Chisoni Chifukwa cha Imfa ya Bambo Kapena Mayi Anu?

Zimakhala zothetsa nzeru kwambiri bambo kapena mayi ako akamwalira. Kodi wachinyamata amene bambo kapena mayi anamwalira, angatani ngati ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya kholo lakelo?

Ndingatani Ngati Ndili Ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

Zinthu 4 zomwe zingakuthandizeni ngati muli ndi maganizo oona kuti bola kungofa.

Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?

Anthu ambiri amene akuvutitsidwa amaona kuti palibe chimene angachite. Nkhaniyi ikufotokoza zimene mungachite kuti anthu asiye kukuvutitsani.

Ndingatani Ngati Anzanga Amandivutitsa?

Simungathe kuchititsa kuti anthu asamakuvutitseni, koma mungathe kusintha mmene mumawayankhira.

Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani?

Onerani vidiyoyi kuti mudziwe chifukwa chake anthu amavutitsa anzawo komanso zimene mungachite kuti asiye kukuvutitsani.

Ndingatani Ngati Anthu Ena Amandivutitsa pa Intaneti?

Zimene muyenera kuchita komanso zimene mungachite kuti mudziteteze.

Zimene Mungachite Kuti Anthu Asiye Kukuvutitsani pa Intaneti

Tsambali likuthandizani kuzindikira ubwino ndi mavuto a njira zosiyanasiyana komanso kuti muthe kudziwa zoyenera kuchita kuti winawake asamakuvutitseni pa Intaneti.

Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Moyo Wanga?

Malo ochezera a pa intaneti amakomedwetsa. Mfundo zotsatirazi zikuthandizani kuti muzidziletsa.

Zimene Zingakuthandizeni Mukatha Msinkhu

Werengani kuti mudziwe zimene zimachitika pa nthawiyi komanso zimene zingakuthandizeni.

N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?

Achinyamata ena ali ndi vuto lodzivulaza mwadala. Ngati muli ndi khalidwe limeneli, kodi mungatani kuti mulisiye?

Kodi Ineyo Ndingatani Kuti Ndipewe Vuto la Kupanikizika?

Kodi n’chiyani chimayambitsa vuto la kupanikizika? Kodi inunso mumapanikizika kwambiri? Ngati ndi choncho, kodi mungatani kuti muthane ndi vutoli?

Zomwe Zingakuthandizeni Ngati Chibwenzi Chatha

Mfundo zomwe zili mu zochitazi zikuthandizani kuti muzisangalalabe ngakhale kuti chibwenzi chatha.

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Nkhanza za Kugonana?​—Gawo 2: Zimene Mungachite Ngati Munachitidwapo Nkhanza Zotere

Werengani zimene zinathandiza anthu omwe anachitidwa nkhanza zokhudza kugonana kuti azikhala osangalala.