Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Nthawi Yopuma

Zosangalatsa zingakuthandizeni kupeza mphamvu kapenanso zingakutopetseni. Onani mmene mungagwiritsire ntchito mwanzeru nthawi yanu yopuma kuti mupindule nayo kwambiri.

Kodi Palibe Vuto Ngati Nditamangomvera Nyimbo Iliyonse?

Popeza nyimbo ndi zamphamvu, nkhaniyi ingakuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti muzisankha nyimbo mwanzeru.

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Kusewera Magemu a Pazipangizo Zamakono?

Mwina simunaganizirepo ubwino komanso kuipa kosewera magemu.

Magemu Amene Ndimasewera pa Zipangizo Zamakono

Mafunsowa angakuthandizeni kudziwa ngati magemu amene mumasewera ali abwino kapena ayi.

Kodi Mumakonda Kusewera Magemu a Pakompyuta?

Kusewera magemu a pakompyuta kungakhale kosangalatsa koma kulinso ndi mavuto ake. Kodi mungatani kuti mupewe mavuto ake n’kumachita zinthu zopindulitsadi?

Zimene Muyenera Kudziwa pa Nkhani Yochita Masewera

Masewera angakuthandizeni kukhala ndi maluso enaake, monga kuchita zinthu mogwirizana ndi anthu ena. Kodi masewera muyenera kuwaika m’gulu la zinthu zofunika kwambiri pa moyo wanu?

Kodi Ndiyenera Kuganizira Mfundo Ziti pa Nkhani ya Masewera?

Muyenera kuganizira masewera amene mumachita, zimene mumachita posewerapo ndiponso kuchuluka kwa nthawi imene mumachita masewerawo.

Kodi Mumakonda Masewera Oika Moyo Pangozi?

Achinyamata ambiri amafuna kudziwa ngati angakwanitse kuchita masewera enaake ngakhale kuti nthawi zina zingaike moyo wawo pangozi. Kodi nanunso zimenezi zimakuchitikirani?

Kugawa Nthawi Yochita Zosangalatsa Komanso Zofunika

Kodi mumakonda kuyamba ndi “miyala” kapena “mchenga”?

Ndingatani Kuti Ndizigawa Bwino Nthawi Yanga?

Mfundo 5 zomwe zingakuthandizeni kuti muzipewa kuwononga nthawi yanu.

Ndingatani Ngati Ndaboweka?

Kodi zipangizo zamakono zingakuthandizeni pa nkhaniyi? Nanga kodi zinthu zingamakuyendereni potengera mmene mumaonera zinthu?

Kodi Kuchita Zamatsenga Kuli ndi Vuto Lililonse?

Anthu ambiri masiku ano amachita chidwi ndi zamatsenga, ziwanda, mavampaya, mizukwa ndi ufiti. Kodi pali vuto lililonse ndi zinthu zimenezi?

N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Samandilola Kusangalalako?

Onani chifukwa chake makolo anu sangakuloleni kuchita zomwe mwapempha komanso zimene mungachite kuti nthawi zambiri azikuvomerezani kuchita zomwe mwapempha.