Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Thanzi Lanu

Onani zomwe mungachite kuti mukhale ndi thanzi labwino kapenanso kuti mupirire matenda ovuta. Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wanu, Baibulo lili ndi malangizo omwe angakuthandizeni kwambiri.

Mavuto

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu? (Gawo 1)

Achinyamata 4 akufotokoza zimene zikuwathandiza kupirira matenda awo kuti asamangokhalira kudandaula.

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?—Gawo 2

Werengani zimene achinyamata ena anachita kuti athe kupirira matenda aakulu komanso kuti azikhalabe osangalala.

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?—Gawo 3

Zitsanzo za achinyamata atatu zingakuthandizeni kupirira matenda.

Zimene Zingakuthandizeni Mukatha Msinkhu

Werengani kuti mudziwe zimene zimachitika pa nthawiyi komanso zimene zingakuthandizeni.

Zomwe Zingawononge Thanzi Lanu

Kodi Ineyo Ndingatani Kuti Ndipewe Vuto la Kupanikizika?

Kodi n’chiyani chimayambitsa vuto la kupanikizika? Kodi inunso mumapanikizika kwambiri? Ngati ndi choncho, kodi mungatani kuti muthane ndi vutoli?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani pa Nkhani Yomwa Mowa?

Onani mmene mungapewere kuphwanya malamulo, kuononga mbiri yanu, kuchitidwa nkhanza zokhudza kugonana, kukonda kwambiri mowa komanso imfa.

Kodi Mungatani pa Nkhani ya Mowa?

Zoti muchitezi zikuthandizani kudziwa zoyenera kuchita ngati anzanu akukukakamizani kuti mumwe mowa.

Ganizirani Zimene Zingachitike Ngati Mutamwa Mowa

Kuchita zinthu chifukwa cha mowa, anthu ambiri amanena kapena kuchita zinthu zimene pambuyo pake amanong’oneza nazo bondo. Kodi mungatani kuti mupewe mavuto amene amakhalapo chifukwa chomwa kwambiri mowa?

Musawononge Moyo Wanu Chifukwa cha Kusuta

Anthu ambiri amasuta kapena kuvepa. Komabe ena asiya ndipo enanso akufunitsitsa kusiya. N’chifukwa chiyani akuchita zimenezi? Kodi kusuta kungawonongedi moyo wanu?

Zomwe Ndiyenera Kudziwa pa Nkhani Yosuta Kapena Kuvepa

Zinthu zimene anthu otchuka kapena anzako amaziona ngati ‘zosangalatsa’ sizikhala zosangalatsa kwenikweni koma amakhala akudziputira mavuto aakulu. Dziwani mavuto amene amabwera chifukwa cha kuvepa komanso mmene mungawapewere.

Moyo Wathanzi

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigona Mokwanira?

Mfundo 7 zimene zingakuthandizeni kuti muzigona mokwanira.

Ndingatani Kuti Ndizikonda Masewera Olimbitsa Thupi?

Kuwonjezera pa kukhala ndi thanzi labwino, kodi masewera olimbitsa thupi angakuthandizeninso bwanji?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizidya Zakudya Zopatsa Thanzi?

Munthu amene sadya zakudya zopatsa thanzi ali wamng’ono amachitanso zomwezo akadzakula. Choncho ndibwino kuti muzikhala ndi chizolowezi chomadya zakudya zopatsa thanzi panopa.

Ndingatani Kuti Ndichepetse Thupi?

Ngati mukufuna kuchepetsa thupi si bwino kumasala zakudya zina, mukhoza kungosintha zinthu zina pa moyo wanu.